2 Akorinto 10 BL92

Ulamuliro wa Paulo mtumwi

1 Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Kristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzicepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;

2 koma ndipempha kuti pokhala ndiri pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tirikuyendayenda monga mwa thupi,

3 Pakuti pakuyendayenda m'thupi, siticita nkhondo monga mwa thupi,

4 (pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);

5 ndi kugwetsa matsutsano, ndi cokwezeka conse cimene cidzikweza pokana ddziwitso ca Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu;

6 ndi kukhala okonzeka Irubwezera cilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.

7 Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Kristu, ayesere icinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Kristu, koteronso ife.

8 Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kocurukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye ku kumangirira, ndipo si ku kugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;

9 kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa akalatawo.

10 Pakuti, akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lace ngofoka, ndi mau ace ngacabe.

11 Wotereyo ayese ici kuti monga tiri ife ndi mau mwa akalata, pokhala palibe ife, tiri oterenso m'macitidwe pokhala tiri pomwepo.

12 Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzibvomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwookha, alibe nzeru.

13 Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa cilekelezero cimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.

14 Pakuti sitinyanyampiradi tokha, monga ngati sitinafikira kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mu Uthenga Wabwino wa Kristu:

15 osadzitamandira popitirira muyeso mwa macititso a ena; koma tiri naco ciyembekezo kuti pakukula cikhulupiriro canu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa cilekezero cathu kwa kucurukira,

16 kukalalikira Uthenga Wabwino m'tsogolo mwace mwa inu, sikudzitamandira mwa cilekezero ca wina, ndi zinthu zokonzeka kale.

17 Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye;

18 pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wobvomerezeka.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13