25 Koma popeza cadza cikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi.
26 3 Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa cikhulupiriro ca mwa Yesu Kristu.
27 4 Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.
28 5 Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; 6 pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.
29 Koma ngati muli a Kristu, muli mbeu ya Abrahamu, 7 nyumba monga mwa Lonjezano.