3 Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi?
4 Kodi mudamva zowawa zambiri zotere kwacabe? ngatitu kwacabe.
5 Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nacita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi nchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa cikhulupiriro?
6 Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye cilungamo,
7 cotero zindikirani kuti iwo a cikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.
8 Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi cikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.
9 Kotero kuti iwo a cikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo,