1 Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; cifukwa cace cirimikani, musakodwenso ndi gori la ukapolo.
2 Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Kristu simudzapindula naye kanthu.
3 Ndicitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kucita cilamulo conse.
4 Mulibe kanthu ndi Kristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana naco cisomo.
5 Pakuti ife mwa Mzimu, kucokera m'cikhulupiriro, tilindira ciyembekezo ca cilungamo,
6 Pakuti mwa Kristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu cikhulupiriro cakucititsa mwa cikondi.