3 Ndicitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kucita cilamulo conse.
4 Mulibe kanthu ndi Kristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana naco cisomo.
5 Pakuti ife mwa Mzimu, kucokera m'cikhulupiriro, tilindira ciyembekezo ca cilungamo,
6 Pakuti mwa Kristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu cikhulupiriro cakucititsa mwa cikondi.
7 Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere coonadi?
8 Kukopa kumene sikucokera kwa iye anakuitanani.
9 Cotupitsa pang'ono citupitsa mtanda wonse.