1 Zicokera kuti nkhondo, zicokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizicokera ku zikhumbitso zanu zocita nkhondo m'ziwalo zanu?
2 Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimucita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimucita nkhondo; mulibe kanthu, cifukwa simupempha.
3 Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukacimwaze pocita zikhumbitso zanu.
4 Akazi acigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uti udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.
5 Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena cabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kucita nsanje?
6 Koma apatsa cisomo coposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo odzicepetsa.
7 Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.