5 Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena cabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kucita nsanje?
6 Koma apatsa cisomo coposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo odzicepetsa.
7 Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.
8 Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu, Sambani m'manja, ocimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
9 Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi cimwemwe canu cisanduke cisoni.
10 Dzicepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.
11 Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wace, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suliwocita lamulo, komatu woweruza.