5 Amaliwongo ace asanduka akuru ace, adani ace napindula;Pakuti Yehova wamsautsa pocuruka zolakwa zace;Ana ace ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ace.
6 Ulemu wace wonse wamcokera mwana wamkazi wa Ziyoni;Akalonga ace asanduka nswala zosapeza busa,Anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompitikitsa.
7 M'masiku a msauko wace ndi kusocera kwaceYerusalemu ukumbukira zokondweretsa zace zonse zacikhalire;Pogwidwa anthu ace ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa,Adaniwo anamuona naseka mwacipongwe mabwinja ace.
8 Yerusalemu wacimwa kwambiri; cifukwa cace wasanduka cinthu conyansa;Onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamarisece;Inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.
9 Udio wace unali m'nsaru zace; sunakumbukira citsiriziro cace;Cifukwa cace watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza;Taonani Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuzayekha.
10 Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zace zonse;Pakuti waona amitundu atalowa m'malo ace opatulika,Amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.
11 Anthu ace onse ausa moyo nafunafuna mkate;Ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao;Taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.