1 Ha! golidi wagugadi; golidi woona woposa wasandulika;Miyala ya malo opatulika yakhutulidwa pa malekezero a makwalalaonse.
2 Ana a Ziyoni a mtengo wapatari, olingana ndi golidi woyengetsa,Angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.
3 Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao;Koma mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga wasanduka wankhanza, ngati nthiwatiwa za m'cipululu.
4 Lilime la mwana woyamwa limamatira kumalakalaka kwace ndi ludzu;Ana ang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.
5 Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m'makwalala;Omwe analeredwa nabvekedwa mlangali afungatira madzala.
6 Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga, ikula koposa cimo la Sodomu,Umene unapasuka m'kamphindi, anthu osaucitira kanthu.