1 NYIMBO yoposa, ndiyo ya Solomo.
2 Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwace;Pakuti cikondi cako ciposa vinyo.
3 Mafuta ako anunkhira bwino;Dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa;Cifukwa cace anamwali akukonda.
4 Undikoke; tikuthamangire;Mfumu yandilowetsa m'zipinda zace:Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe.Tidzachula cikondi cako koposa vinyo:Akukonda molungama.
5 Wakuda ine, koma wokongola,Ana akazinu a ku Yerusalemu,Ngati mahema a Kedara,Ngati nsaru zociriga za Solomo.
6 Musayang'ane pa ine, pakuti ndada,Pakuti dzuwa landidetsa.Ana amuna a amai anandikwiyira,Anandisungitsa minda yamipesa;Koma munda wanga wanga wamipesa sindinausunga.
7 Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda,Umaweta kuti gulu lako?Umaligonetsa kuti pakati pa usana?Pakuti ndikhalirenji ngati wosoceraPambali pa magulu a anzako?