Nyimbo 1 BL92

Mkwatibwi anena ndi ana a Yerusalemu za mkwati

1 NYIMBO yoposa, ndiyo ya Solomo.

2 Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwace;Pakuti cikondi cako ciposa vinyo.

3 Mafuta ako anunkhira bwino;Dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa;Cifukwa cace anamwali akukonda.

4 Undikoke; tikuthamangire;Mfumu yandilowetsa m'zipinda zace:Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe.Tidzachula cikondi cako koposa vinyo:Akukonda molungama.

5 Wakuda ine, koma wokongola,Ana akazinu a ku Yerusalemu,Ngati mahema a Kedara,Ngati nsaru zociriga za Solomo.

6 Musayang'ane pa ine, pakuti ndada,Pakuti dzuwa landidetsa.Ana amuna a amai anandikwiyira,Anandisungitsa minda yamipesa;Koma munda wanga wanga wamipesa sindinausunga.

7 Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda,Umaweta kuti gulu lako?Umaligonetsa kuti pakati pa usana?Pakuti ndikhalirenji ngati wosoceraPambali pa magulu a anzako?

8 Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola,Dzituruka kukalondola bande la gululo,Nukawete ana a mbuzi zako pambali pa mahema a abusa.

Mkwati ndi mkwatibwi akambirana za cikondano cao

9 Ndakulinganiza, wokondedwa wanga mnyamatawe,Ngati akavalo a magareta a Farao.

10 Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi,Ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira.

11 Tidzakupangira nkhata zagolidiNdi njumu zasiliva.

12 Pokhala mfumu podyera pace,Mphoka yanga inanunkhira.

13 Wokondedwa wanga mnyamatayo ali kwa ine ngati thumba la nipa,Logona pakati pa maere anga.

14 Wokondedwa wanga ali kwa ine ngati cipukutu ca maluwa ofiiraM'minda yamipesa ya ku Engedi.

15 Taona, wakongolatu, bwenzi langa; namwaliwe taona, wakongola,Maso ako akunga a nkhunda.

16 Taona, wakongolatu, bwenzi langa, mnyamatawe, inde, wakongoletsa;Pogona pathu mpa msipu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8