Mlaliki 12 BL92

1 Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo;

2 ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula;

3 tsikulo omwe asunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzawerama, akupera nadzaleka poperewera, omwe ayang'ana pamazenera nadzadetsedwa;

4 pa khomo lakunja padzatsekeka; potsika mau akupera, wina nanyamuka polira mbalame, ndipo akazi onse akuyimba sadzamveka bwino;

5 inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsya; mciu nudzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;

6 cingwe casiliva cisanaduke, ngakhale mbale yagolidi isanasweke, ngakhale mtsuko usanaphwanyike kukasupe, ngakhale njinga yotungira madzi isanatyoke kucitsime;

7 pfumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.

8 Cabe zacabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi cabe.

Zoyenera munthu ndizo kuopa Mulungu ndi kusunga malamulo ace

9 Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anachera makutu nafunafuna nalongosolamiyambiyambiri.

10 Mlalikiyo anasanthula akapeze mau okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mau oona.

11 Mau a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mau amene mbusa mmodzi awapatsa mau ao akunga misomali yokhomedwa zolimba.

12 Pamodzi ndi izi, mwananga, tacenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.

13 Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ace; pakuti coyenera anthu onse ndi ici.

14 Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zocita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12