Mlaliki 5 BL92

Malangizo osiyana akuwasamalira anthu m'moyo uno

1 Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zirikucimwa.

2 Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; cifukwa cace mau ako akhale owerengeka.

3 Pakuti loto lafika mwakucuruka nchito; ndipo mau a citsiru mwakucuruka maneno.

4 Utawinda ciwindo kwa Mulungu, usacedwe kucicita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; cita comwe unaciwindaco.

5 Kusawinda kupambana kuwinda osacita,

6 Usalole m'kamwa mwako mucimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako cifukwa ninji, naononge nchito ya manja ako?

7 Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zacabe motero mocuruka mau; koma dziopa Mulungu.

8 Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kucotsa cilungamo ndi ciweruzo mwaciwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkuru wopambana asamalira; ndipo alipo akuru ena oposa amenewo.

9 Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza.

10 Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda cuma sadzakhuta phindu; icinso ndi cabe.

11 Pocuruka katundu, akudyapo acurukanso; nanga apindulira eni ace ciani, koma kungopenyera ndi maso ao?

12 Tulo ta munthu wogwira nchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.

13 Pali coipa cobvuta ndaciona kunja kuno, ndico, cuma cirikupweteka eni ace pocikundika;

14 koma cumaco cionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m'dzanja lace mulibe kanthu.

15 Monga anaturuka m'mimba ya amace, adzabweranso kupita wamarisece, monga anadza osatenga kanthu pa nchito zace, kakunyamula m'dzanja lace.

16 Icinso ndi coipa cowawa, cakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa cabe adzaona phindu lanji?

17 Inde masiku ace onse amadya mumdima, nizimcurukira cisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.

18 Taonani, comwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi nchito zace zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wace umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lace limeneli.

19 Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa cuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lace ndi kukondwera ndi nchito zace; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.

20 Pakuti sadzakumbukira masiku a moyo wace kwambiri; cifukwa Mulungu ambvomereza m'cimwemwe ca mtima wace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12