Mlaliki 7 BL92

Kumva zowawa nkokoma, nzeru ndi kudziletsa momwemo

1 Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.

2 Kunka ku nyumba ya maliro kupambana kunka ku nyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.

3 Cisoni ciposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.

4 Mtima wa anzeru uli m'nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m'nyumba ya kuseka.

5 Kumva cidzudzulo ca anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru.

6 Pakuti kuseka kwa citsiru kunga minga irikutetheka pansi pa mphika; icinso ndi cabe.

7 Indetu nsautso iyarutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima.

8 Citsiriziro ca kanthu ciposa ciyambi cace; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima.

9 Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'cifuwa ca zitsiru.

10 Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.

11 Nzeru iri yabwino pamodzi ndi colowa; akuona dzuwa apindula nayo.

12 Pakuti nzeru icinjiriza monga ndalama zicinjiriza; koma kudziwa kupambana, cifukwa nzeru isunga moyo wa eni ace.

13 Tapenya nchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa comwe iye anacikhotetsa?

14 Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ici pambali pa cinzace, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.

15 Ndaona zonsezi masiku anga acabe; pali wolungama angofa m'cilungamo cace, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwace.

16 Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha?

17 Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa, uferenji nthawi yako isanafike?

18 Kuli kwabwino kugwira ici; indetu, usacotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzaturuka monsemo.

19 Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akuru khumi akulamulira m'mudzi.

20 Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene acita zabwino osacimwa.

21 Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera;

22 pakuti kawiri kawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.

23 Ndayesa zonsezi ndi nzeru; ndinati, Ndidzakhala wanzeru, koma inanditarikira.

24 Cakutari ndi cakuyadi adzacipeza ndani?

25 Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udio ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;

26 ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wace ukunga maukonde, manja ace ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wocimwa adzagwidwa naye.

27 Taonani, ici ndacipeza, ati Mlalikiyo, m'kuphatikiza cinthu cina ndi cinzace, ndikazindikire malongosoledwe ao;

28 comwe moyo wanga ucifuna cifunire, koma osacipezai ndi ici, mwamuna mmodzi mwa cikwi ndinampezadi, koma mkazitu mwa onsewo sindinampeza.

29 Taonani, ici cokha ndacipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundu mitundu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12