Mlaliki 4 BL92

Matsoka ndi mabvuto a moyo uno

1 Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimacitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.

2 Ndipo ndinatama akufa atatha kufa kupambana amoyo omwe alipobe;

3 inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone nchito yoipa yocitidwa kunja kuno.

4 Ndiponso ndinapenyera mabvuto onse ndi nchito zonse zompindulira bwino, kuti cifukwa ca zimenezi anansi ace acitira munthu nsanje. Icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.

5 Citsiru cimanga manja ace, nicidya nyama yace yace.

6 Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti tho pali bvuto ndi kungosautsa mtima.

7 Pamenepo ndinabwera ndi kupenyera zacabe kunja kuno.

8 Pali mmodzi palibe waciwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma nchito yace yonse iribe citsiriziro, ngakhale diso lace silikhuta cuma. Samati, Ndigwira nchito ndi kumana moyo wanga zabwino cifukwa ca yani? Icinso ndi cabe, inde, bvuto lalikuru.

9 Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m'nchito zao.

10 Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzace; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.

11 Ndiponso awiri akagona limodzi afunditsana; koma mmodzi pa yekha kodi adzafunditsidwa bwanji?

12 Ndipo wina akamlaka mmodziyo, awiri adzacirimika; ndipo cingwe ca nkhosi zitatu siciduka msanga.

13 Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.

14 Pakuti aturuka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lace asauka.

15 Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, waciwiri, amene adzalowa m'malo mwace.

16 Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Icinso ndi cabe nicisautsa mtima.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12