Mlaliki 8 BL92

Langizo la kumvera mfumu

1 Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yace, kuduwa kwa nkhope yace ndi kusanduka.

2 Nditi, Sunga mau a mfumu, makamaka m'kulumbira Mulungu.

3 Usakangaze kumcokera; usaumirire kanthu koipa; pakuti iyeyo amacita comwe cimkonda.

4 Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi ucita ciani?

5 Wosunga cilamulo sadzadziwa kanthu koipa; ndipo mtima wa munthu wanzeru udziwa nyengo ndi maweruzo;

6 pakuti kanthu kali konse kali ndi nthawi yace ndi ciweruzo cace; popeza zoipa za munthu zimcurukira;

7 pakuti sadziwa cimene cidzakhala; pakuti ndani angamuuze nthawi yakuti cidzacitidwa?

8 Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udio sudzapulumutsa akuzolowerana nao.

9 Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga nchito zonse zicitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzace pomlamulira.

Woipa salangidwa pakucita pomwepo; mwina wolungama aona nsautso

10 Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anacita zolungama anacokera ku malo opatulika a ku mudzi nawaiwala; icinso ndi cabe.

11 Popeza sambwezera coipa cace posacedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kucita zoipa.

12 Angakhale wocimwa acita zoipa zambirimbiri, masiku ace ndi kucuruka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pace adzapeza bwino;

13 koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ace ngati mthunzi; cifukwa saopa pamaso pa Mulungu.

14 Pali cinthu cacabe cimacitidwa pansi pano; cakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera nchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera nchito za olungama, Ndinati, Icinso ndi cabe.

15 Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m'bvuto lace masiku onse a moyo wace umene Mulungu wampatsa pansi pano.

16 Pompo ndinapereka mtima wanga kudziwa nzeru, ndi kupenya nchito zicitidwa pansi pano; kuti anthu saona tulo konse ndi maso ao ngakhale usana ngakhale usiku;

17 pamenepo ndinaona nchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole nchito ziciddwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12