1 Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi cimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, icinso ndi cabe.
2 Ndinati, Kuseka ndi misala; ndi cimwemwe kodi cicita ciani?
3 Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire cabwinoco ca ana a anthu nciani cimene azicicita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.
4 Ndinadzipangira zazikuru; ndinadzimangira nyumba; ndi kunka mipesa;
5 ndinakonza mphanie ndi minda yanga, ndi kuokamo mitengo ya zipatso za mitundu mitundu;
6 ndinadzipangira ndekha matamanda a madzi akuthirira madzi m'nkhalango momeramo mitengo;
7 ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikuru ndi zazing'ono kupambana onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine;
8 ndinakundikanso siliva ndi golidi ndi cuma ca mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuyimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoyimbira za mitundu mitundu.
9 Ndinakula cikulire kupambana onse anali m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe.
10 Ndipo ciri conse maso anga anacifuna sindinawamana; sindinakaniza mtima wanga cimwemwe ciri conse pakuti mtima wanga unakondwera ndi nchito zanga zonse; gawo langa la m'nchito zanga zonse ndi limeneli.
11 Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi nchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zacabecabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.
12 Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angacite ciani? Si comwe cinacitidwa kale.
13 Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.
14 Wanzeru maso ace ali m'mutu wace, koma citsiru ciyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti comwe ciwagwera onsewo ndi cimodzi.
15 Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Comwe cigwera citsiru nanenso cindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti icinso ndi cabe.
16 Pakuti wanzerusaposa citsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo, Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati citsirutu.
17 Cifukwa cace ndinada moyo; pakuti nchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
18 Ndipo ndinada nchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno; pakuti ndidzamsiyira izo munthu wina amene adzanditsata.
19 Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena citsiru? Koma adzalamulira nchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Icinso ndi cabe.
20 Ndipo ndinatembenuka ndi kukhululuka za nchito zanga zonse ndasauka nazo kunja kuno.
21 Pakuti pali munthu wina agwira nchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lace kwa munthu amene sanagwirapo nchito. Icinso ndi cabe ndi coipa cacikuru.
22 Pakuti munthu ali ndi ciani m'nchito zace zonse, ndi m'kusauka kwa mtima wace amasauka nazozo kunja kuno?
23 Pakuti masiku ace onse ndi zisoni, bvuto lace ndi kumliritsa; ngakhale usiku mtima wace supuma. Icinso ndi cabe.
24 Kodi si cabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wace, zabwino m'nchito yace? icinso ndinacizindikira kuti cicokera ku dzanja la Mulungu.
25 Pakuti ndani angadye ndi kufulumirako, koposa ine.
26 Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi cidziwitso ndi cimwemwe; koma wocimwa amlawitsa bvuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.