Mlaliki 10 BL92

Kupusa kusautsa kwambiri

1 Nchenche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; comweco kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene achuka cifukwa ca nzeru ndi ulemu.

2 Wanzeru, mtima wace uli ku dzanja lace lamanja; koma citsiru, mtima wace kulamanzere.

3 Inde, poyendanso citsiru panjira, nzeru yace imthera ndipo angoti kwa onse kuti, Ndine citsiru.

4 Ngati mkuru akukwiyira, usasiye malo ako; cifukwa cifatso cipembedza utacimwa kwambiri.

5 Pali coipa ndaciona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkuru;

6 utsiru ukhazikika pamwamba penipeni, ndipo olemera angokhala mwamanyazi.

7 Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, ndi mafumu, alikuyenda pansi ngati akapolo.

8 Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma.

9 Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema.

10 Citsulo cikakhala cosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pocenjeza.

11 Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.

12 Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga cisomo; koma milomo ya citsiru idzacimeza.

13 Ciyambi ca mau a m'kamwa mwace ndi utsiru; ndipo cimariziro ca m'kamwa mwace ndi misala yoipa,

14 Citsiru cicurukitsanso mau; koma munthu sadziwa cimene cidzaoneka; ndipo ndani angamuuze comwe cidzakhala m'tsogolo mwace?

15 Nchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sicidziwa kunka kumudzi.

16 Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa!

17 Mwai kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana wa aufulu, ndipo akalonga ako adya pa nthawi yoyenera akalimbe osati akaledzere ai.

18 Tsindwi litewa ndi mphwai za eni ace; nyumba nidontha ndi ulesi wa manja.

19 Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zibvomera zonse.

20 Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'cipinda cogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo couluka ndi mapiko cidzamveketsa zonenazo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12