1 MAU a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya m'Yerusalemu.
2 Zacabecabe, ati Mlaliki; zacabecabe zonse ndi cabe.
3 Kodi nchito zace zonse munthu asauka nazo zimpindulira ciani?
4 Mbadwo wina opita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse,
5 inde dzuwa lituruka, nililowa, nilifulumira komwe linaturukako.
6 Kulowa kumwela ndi kuzungulira: kumpoto zungulire zungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ace.
7 Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.
8 Zinthu zonse zilemetsa; munthu sakhoza kuzifotokoza; maso sakhuta m'kuona, ndi makutu sakhuta m'kumva.
9 Comwe cinaoneka cidzaonekanso; ndi comwe cinacitidwa cidzacitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano.
10 Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.
11 Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zirinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.
12 Ine Mlaliki ndinali mfumu ya: Israyeli m'Yerusalemu.
13 Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimacitidwa pansi pa thambo; nchito yobvuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.
14 Ndaona nchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
15 Cokhotakhota sicingaongokenso; ndipo coperewera sicingawerengedwe.
16 Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi cidziwitso.
17 Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti icinso cingosautsa mtima.
18 Pakuti m'nzeru yambiri muli cisoni cambiri; ndi yemwe aenjezera cidziwitso aenjezera zowawa.