Miyambi 31 BL92

Malangizo a mai wa Lemueli

1 Mau a Lemueli mfumu, uthenga umene amace anamphunzitsa.

2 Ciani mwananga, Ciani mwana wa mimba yanga?Ciani mwana wa zowinda zanga?

3 Musapereke mphamvu yako kwa akazi,Ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu.

4 Mafumu, Lemueli, mafumu sayenera kumwa vinyo;Akalonga sayenera kunena, Cakumwa caukali ciri kuti?

5 Kuti angamwe, naiwale malamulo,Naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.

6 Wofuna kufa umpatse cakumwa caukali,Ndi vinyo kwa owawa mtima;

7 Amwe, narwale umphawi wace, Osakumbukiranso bvuto lace.

8 Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula,Ndi mlandu wa amasiye onse.

9 Tsegula pakamwa pako,Nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.

10 Mkazi wangwiro ndani angampeze?Pakuti mtengo wace uposa ngale.

11 Mtima wa mwamuna wace umkhulupirira,Sadzasowa phindu.

12 Mkaziyo amcitira zabwino, si zoipa,Masiku onse a moyo wace.

13 Afuna ubweya ndi thonje,Nacita mofunitsa ndi manja ace.

14 Akunga zombo za malonda;Nakatenga zakudya zace kutari.

15 Aukanso kusanace,Napatsa banja lace zakudya, nagawira adzakazi ace nchito.

16 Asinkhasinkha za munda, naugula;Naoka mipesa ndi zipatso za manja ace.

17 Amanga m'cuuno mwace ndi mphamvu,Nalimbitsa mikono yace,

18 Azindikira kuti malonda ace ampindulira;Nyali yace sizima usiku.

19 Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lace,Nafumbata mtengo wace.

20 Aolowera cikhato cace osauka;Natambasulira aumphawi manja ace.

21 Saopera banja lace cipale cofewa;Pakuti banja lace lonse libvala mlangali.

22 Adzipangira zimbwi zamaangamaanga;Nabvala bafuta ndi guta woti biriwiri.

23 Mwamuna wace adziwika kubwalo,Pokhala pakati pa akuru a dziko.

24 Asoka maraya abafuta, nawagulitsa;Napereka mipango kwa wogulitsa malonda.

25 Abvala mphamvu ndi ulemu;Nangoseka nthawi ya m'tsogolo.

26 Atsegula pakamwa pace ndi nzeru,Ndipo cilangizo ca cifundo ciri pa lilime lace.

27 Ayang'anira mayendedwe a banja lace,Sadya zakudya za ulesi.

28 Anace adzanyamuka, nadzamucha wodala;Mwamuna wace namtama, nati,

29 Ana akazi ambiri anacita mwangwiro,Koma iwe uposa onsewo.

30 Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi cabe;Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.

31 Mumpatse zipatso za manja ace; Ndi nchito zace zimtame kubwalo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31