Miyambi 23 BL92

1 Pamene ukhala ulinkudya ndi mkuru,Zikumbukira ameneyo ali pamaso pako;

2 Nuike mpeni pakhosi pako,Ngati uli wadyera.

3 Usakhumbe zolongosoka zace;Pokhala zakudya zonyenga.

4 Usadzitopetse kuti ulemere;Leka nzeru yako yako.

5 Kodi upenyeranji cimene kulibe?Pakuti cuma cunera mapiko,Ngati mphungu youluka mumlengalenga.

6 Usadye zakudya zace za wa maso ankhwenzule,Ngakhale kukhumba zolongosoka zace;

7 Pakuti monga asinkha m'kati mwace, ali wotere;Ati kwa iwe, Idya numwe;Koma mtima wace suli pa iwe.

8 Pakuti nthongo imene unaidya udzaisanza,Ndi kutaya mau ako okondweretsa.

9 Usalankhule m'makutu a wopusa;Pakuti adzapeputsa nzeru ya mau ako.

10 Usasunthe cidziwitso cakale ca m'malire;Ngakhale kulowa m'minda ya amasiye;

11 Pakuti Mombolo wao walimba;Adzawanenera mlandu wao pa iwe.

12 Lozetsa mtima wako kumwambo,Ndi makutu ako ku mau a nzeru.

13 Usamane mwana cilango;Pakuti ukammenya ndi ntyole safa ai.

14 Udzammenya ndi ntyole,Nudzapulumutsa moyo wace kunsi kwa manda.

15 Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru,Mtima wanga wa inedi udzakondwa;

16 Imso zanga zidzasangalala,Polankhula milomo yako zoongoka.

17 Mtima wako usacitire nsanje akucimwawo;Koma opabe Yehova tsiku lonse;

18 Pakutitu padzakhala mphotho;Ndipo ciyembekezo cako sicidzalephereka.

19 Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru,Ulunjikitse mtima wako m'njiramo.

20 Usakhale mwa akumwaimwa vinyo,Ndi ankhuli osusuka.

21 Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka;Ndipo kusinza kudzabveka munthu nsanza.

22 Tamvera atate wako anakubala,Usapeputse amako atakalamba.

23 Gula ntheradi, osaigulitsa;Nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.

24 Atate wa wolungama adzasekeradi;Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.

25 Atate wako ndi amako akondwere,Amako wakukubala asekere.

26 Mwananga, undipatse mtima wako,Maso ako akondwere ndi njira zanga,

27 Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya;Ndipo mkazi waciwerewere ndiye mbuna yopapatiza.

28 Pakuti abisalira ngati wacifwamba,Nacurukitsa anthu a ciwembu.

29 Ndani ali ndi cisoni? ndani asauka? ndani ali ndi makangano?Ndani ang'ung'udza? ndani alasidwa cabe? ndani afiira maso?

30 Ngamene acedwa pali vinyo,Napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa.

31 Usayang'ane pavinyo alikufiira.Alikung'azimira m'cikho.Namweka mosalala.

32 Pa citsiriziro cace aluma ngati njoka,Najompha ngati mamba.

33 Maso ako adzaona zacilendo,Mtima wako udzalankhula zokhota.

34 Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja,Pena wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalawa.

35 Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine;Anandikwapula, osamva ine;Ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafuna-funanso vinyoyo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31