Miyambi 11 BL92

1 Muyeso wonyenga unyansa Yehova;Koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.

2 Pakudza kudzikuza padzanso manyazi;Koma nzeru iri ndi odzicepetsa,

3 Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera;Koma kukhota kwa aciwembu kudzawaononga.

4 Cuma sicithandiza tsiku la mkwiyo;Koma cilungamo cipulumutsa kuimfa.

5 Cilungamo ca wangwiro cimaongola njira yace;Koma woipa adzagwa ndi zoipa zace.

6 Cilungamo ca oongoka mtima cidzawapulumutsa;Koma aciwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.

7 Pomwalira woipa cidikiro cace cionongeka;Ciyembekezo ca ucimo cionongeka.

8 Wolungama apulumuka kubvuto;Woipa nalowa m'malo mwace.

9 Wonyoza Mulungu aononga mnzace ndi m'kamwa mwace;Koma olungama adzapulumuka pakudziwa,

10 Olungama akapeza bwino, mudzi usekera;Nupfuula pakuonongeka oipa.

11 Madalitso a olungama akuza mudzi;Koma m'kamwa mwa oipa muupasula.

12 Wopeputsa mnzace asowa nzeru;Koma wozindikira amatonthola.

13 Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi;Koma wokhulupirika mtima abisa mau.

14 Popanda upo wanzeru anthu amagwa;Koma pocuruka aphungu pali cipulumutso.

15 Woperekera mlendo cikole adzaphwetekwapo;Koma wakuda cikole akhala ndi mtendere.

16 Mkazi wodekha agwiritsa ulemu;Aukali nagwiritsa cuma.

17 Wacifundo acitira moyo wace zokoma;Koma wankhanza abvuta nyama yace.

18 Woipa alandira malipiro onyenga;Koma wofesa cilungamo aonadi mphotho,

19 Wolimbikira cilungamo alandira moyo;Koma wolondola zoipa adzipha yekha,

20 Okhota mtima anyansa Yehova;Koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.

21 Zoonadi, wocimwa sadzapulumuka cilango;Koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.

22 Monga cipini cagolidi m'mphuno ya nkhumba,Momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.

23 Cifuniro ca olungama cifikitsa zabwino zokha;Koma ciyembekezo ca oipa mkwiyo.

24 Alipo wogawira, nangolemerabe;Aliponso womana comwe ayenera kupatsa nangosauka.

25 Mtima wa mataya udzalemera;Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.

26 Womana tirigu anthu amtemberera;Koma madalitso adzakhala pamtu pa wogulitsa.

27 Wopwaira ubwino afunitsa cikondwerero;Koma zoipa zidzamfikira wozilondola.

28 Wokhulupmra cuma cace adzagwa;Koma olungama adzaphuka ngati tsamba.

29 Wobvuta banja lace adzalowa m'zomsautsa;Wopusa adzatumikira wanzeru.

30 Cipatso ca wolungama ndi mtengo wa moyo;Ndipo wokola mtima ali wanzeru.

31 Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno;Koposa kotani woipa ndi wocimwa?

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31