Miyambi 25 BL92

Miyambo ya Solomo yosonkhanitsa nthawi ya Hezekiya

1 Iyinso ndiyo miyambo ya SolomoImene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba.

2 Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu;Koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.

3 Pamlengalenga patarika, ndi padziko pakuya,Koma mitima ya mafumu singasanthulike.

4 Cotsera siliva mphala yace,Mmisiri wa ng'anjo aturutsamo mbale;

5 Cotsera woipa pamaso pa mfumu,Mpando wace udzakhazikika m'cilungamo.

6 Usadzitame pamaso pa mfumu,Ngakhale kuima m'malo mwa akuru;

7 Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno,Kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga,Amene maso ako anamuona.

8 Usaturuke mwansontho kukalimbana,Ungalephere pa kutha kwace,Atakucititsa mnzako manyazi.

9 Nena mlandu wako ndi mnzako,Osaulula zinsinsi za mwini;

10 Kuti wakumva angakutonze,Mbiri yako yoipa ndi kusacoka.

11 Mau oyenera a pa nthawi yaceAkunga zipatso zagolidi m'nsengwa zasiliva.

12 Monga phelele lagolidi ndi cipini cagolidi woyengeka,Momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.

13 Monga cisanu ca cipale cofewa pa nthawi ya masika,Momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma;Atsitsimutsa moyo wa ambuyace.

14 Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula,Momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zace monyenga.

15 Cipiriro cipembedza mkuru;Lilime lofatsa lityola pfupa,

16 Wapeza uci kodi? Idyapo wokwanira,Kuti ungakukole, nusanze.

17 Phazi lako lilowe m'nyumba ya mnzako kamodzi kamodzi;Kuti angatope nawe ndi kukuda.

18 Wocitira mnzace umboni wonamaNdiye cibonga, ndi lupanga, ndi mubvi wakuthwa.

19 Kukhulupirira munthu wa ciwembu tsiku latsokaKunga dzino lotyoka ndi phazi loguluka.

20 Monga wobvula maraya tsiku lamphepo,Ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda,Momwemo woyimbira nyimbo munthu wacisoni.

21 Mdani wako akamva njala umdyetse,Akamva ludzu ummwetse madzi,

22 Pakuti udzaunjika makala amoto pamtu pace;Ndipo Yehova adzakupatsa mphotho,

23 Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula;Comweco lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.

24 Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunikaKuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.

25 Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa,Momwemo mau abwino akucokera ku dziko lakutari.

26 Monga kasupe wopondedwa, ndi citsime cobvonongeka,Momwemo wolungama ngati akonjera woipa.

27 Kudya uci wambiri sikuli kwabwino;Comweco kufunafuna ulemu wako wako sikuli ulemu.

28 Wosalamulira mtima waceAkunga mudzi wopasuka wopanda linga,

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31