Miyambi 24 BL92

1 Usacitire nsanje anthu oipa, Ngakhale kufuna kukhala nao;

2 Pakuti mtima wao ulingalira za cionongeko;Milomo yao ilankhula za mphulupulu.

3 Nzeru imangitsa nyumba;Luntha liikhazikitsa.

4 Kudziwa kudzaza zipinda zaceNdi cuma conse cofunika ca mtengo wace.

5 Mwamuna wanzeru ngwamphamvu;Munthu wodziwa ankabe nalimba.

6 Pakuti udzaponya nkhondo yako ndi upo,Ndi kupulumuka pocuruka aphungu,

7 Nzeru itarikira citsiru;Satsegula pakamwa kubwalo.

8 Wolingalira zakucita zoipaAnthu adzamcha waciwembu.

9 Maganizo opusa ndiwo cimo;Wonyoza anyansa anthu.

10 Ukalefuka tsiku la tsokaMphamvu yako icepa.

11 Omwe atengedwa kuti akafe, uwapulumutse;Omwe ati aphedwe, usaleke kuwalanditsa.

12 Ukanena, Taonani, sitinadziwa cimeneci;Kodi woyesa mitima sacizindikira ici?Ndi wosunga moyo wako kodi sacidziwa?Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa macitidwe ace?

13 Mwananga, idya uci pakuti ngwabwino,Ndi cisa cace citsekemera m'kamwamwako;

14 Potero udzadziwa kuti nzeru iri yotero m'moyo wako;Ngati waipeza padzakhala mphotho,Ndipo ciyembekezo cako sicidzalephereka.

15 Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama;Usapasule popuma iyepo.

16 Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso;Koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.

17 Usakondwere pakugwa mdani wako;Mtima wako usasekere pokhumudwa iye;

18 Kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa,Ndi kuleka kumkwiyira.

19 Usabvutike mtima cifukwa ca ocita zoipa;Ngakhale kucitira nsanje amphulupulu;

20 Pakuti woipayo sadzalandira mphotho;Nyali ya amphulupulu idzazima.

21 Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe,Osadudukira anthu osinthasintha.

22 Pakuti tsoka lao lidzaoneka modzidzimuka;Ndipo ndani adziwa cionongeko ca zaka zao?

23 Izinso ziri za anzeru.Poweruza cetera siliri labwino.

24 Wonenakwa woipa, Wolungama iwe;Magulu a anthu adzamtemberera, mitundu ya anthu idzamkwiyira,

25 Omwe amdzudzula adzasekera,Nadzadalitsika ndithu.

26 Wobwezera mau oongokaApsompsona milomo.

27 Longosola nchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda;Pambuyo pace ndi kumanga nyumba yako.

28 Usacitire mnzako umboni womtsutsa opanda cifukwa;Kodi udzanyenga ndi milomo yako?

29 Usanene, Ndidzamcitira zomwezo anandicitira ine;Ndidzabwereza munthuyo monga mwa macitidwe ace.

30 Ndinapita pa munda wa wolesi,Polima mphesa munthu wosowa nzeru.

31 Taonani, ponsepo panamera minga,Ndi kuwirirapo khwisa;Chinga lace lamiyala ndi kupasuka.

32 Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira,Ndinaona ndi kulandira mwambo.

33 Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono,Kungomanga manja pang'ono m'kugona,

34 Ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala;Ndi kusauka kwako ngati munthu wacikopa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31