Miyambi 14 BL92

1 Mkazi yense wanzeru amanga banja lace;Koma wopusa alipasula ndi manja ace.

2 Woyenda moongoka mtima aopa Yehova;Koma wokhota m'njira yace amnyoza,

3 M'kamwa mwa citsiru muli ntyole ya kudzikuza;Koma milomo ya anzeru Idzawasunga.

4 Popanda zoweta modyera muti see;Koma mphamvu ya ng'ombe icurukitsa phindu.

5 Mboni yokhulupirika sidzanama;Koma mboni yonyenga imalankhula zonama.

6 Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza;Koma wozindikira saona bvuto m'kuphunzira.

7 Pita pamaso pa munthu wopusa,Sudzazindikira milomo yakudziwa.

8 Nzeru ya wocenjera ndiyo yakuti azindikire njira yace;Koma utsiru wa opusa ndiwo cinyengo.

9 Zitsiru zinyoza kuparamula;Koma mwa oongoka mtima muli ciyanjano.

10 Mtima udziwa kuwawa kwace kwace;Mlendo sadudukira ndi cimwemwe cace.

11 Nyumba ya oipa idzapasuka;Koma hema wa oongoka mtima adzakula.

12 Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka;Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa.

13 Ngakhale m'kuseka mtima uwawa;Ndipo matsiriziro a ciphwete ndi cisoni.

14 Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira zace;Koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.

15 Wacibwana akhulupirira mau onse;Koma wocenjera asamalira mayendedwe ace.

16 Wanzeru amaopa nasiya zoipa;Koma wopusa amanyada osatekeseka.

17 Wokangaza kukwiya adzacita utsiru;Ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.

18 Acibwana amalandira colowa ca utsiru;Koma ocenjera amabvala nzeru ngati korona.

19 Oipa amagwadira abwino,Ndi ocimwa pa makomo a olungama.

20 Waumphawi adedwa ndi anzace omwe;Koma akukonda wolemera acuruka.

21 Wonyoza anzace acimwa;Koma wocitira osauka cifundo adala.

22 Kodi oganizira zoipa sasocera?Koma akuganizira zabwino adzalandira cifundo ndi ntheradi.

23 M'nchito zonse muli phindu;Koma kulankhula-lankhula kungopatsa umphawi.

24 Korona wa anzeru ndi cuma cao;Utsiru wa opusa ndiwo utsiru.

25 Mboni yoona imalanditsa miyoyo;Koma wolankhula zonama angonyenga.

26 Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo.

27 Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,Kupatutsa ku misampha ya imfa.

28 Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;Koma popanda anthu kalonga aonongeka.

29 Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;Koma wansontho akuza utsiru.

30 Mtima wabwino ndi moyo wa thupi;Koma nsanje ibvunditsa mafupa.

31 Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wace;Koma wocitira wosauka cifundo amlemekeza.

32 Wocimwa adzakankhidwa m'kuipa kwace;Koma wolungama akhulupirirabe pomwalira,

33 Nzeru ikhalabe m'mtima wa wozindikira,Nidziwika pakati pa opusa.

34 Cilungamo cikuza mtundu wa anthu;Koma cimo licititsa pfuko manyazi.

35 Mfumu ikomera mtima kapolo wocita mwanzeru;Koma idzakwiyira wocititsa manyazi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31