Miyambi 3 BL92

Malangizo a kuopa, kukhulupira, ndi kumvera Yehova

1 Mwananga, usaiwale malamulo anga,Mtima wako usunge malangizo anga;

2 Pakuti adzakuonjezera masiku ambiri,Ndi zaka za moyo ndi mtendere.

3 Cifundo ndi coonadi zisakusiye;Uzimange pakhosi pako;Uzilembe pamtima pako;

4 Motero udzapezakisomo ndi nzeru yabwino,Pamaso pa Mulungu ndi anthu.

5 Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,Osacirikizika pa luntha lako;

6 Umlemekeze m'njira zako zonse,Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

7 Usadziyese wekha wanzeru;Opa Yehova, nupatuke pazoipa;

8 Mitsempha yako idzalandirapo moyo,Ndi mafupa ako uwisi.

9 Lemekeza Yehova ndi cuma cako,Ndi zinthu zako zonse zoyambirira kuca;

10 Motero nkhokwe zako zidzangoti the,Mbiya zako zidzasefuka vinyo.

11 Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova,Ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwace;

12 Pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda;Monga atate mwana amene akondwera naye.

Phindu la Nzeru

13 Wodala ndi wopeza nzeru,Ndi woona luntha;

14 Pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva,Phindu lace liposa golidi woyengeka.

15 Mtengo wace uposa ngale;Ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.

16 Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lace;Cuma ndi ulemu m'dzanja lace lamanzere.

17 Njira zace ziri zokondweretsa,Mayendedwe ace onse ndiwo mtendere.

18 Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira;Wakulumirira ngwodala.

19 Yehova anakhazika dziko ndi nzeru;Naika zamwamba ndi luntha.

20 Zakuya zinang'ambika ndi kudziwakwace;Thambo ligwetsa mame.

21 Mwananga, zisacokere ku maso ako;Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;

22 Ndipo mtima wako udzatengapo moyo,Ndi khosi lako cisomo.

23 Pompo udzayenda m'njira yako osaopa,Osapunthwa phazi lako.

24 Ukagona, sudzacita mantha;Udzagona tulo tokondweretsa.

25 Usaope zoopsya zodzidzimutsa,Ngakhale zikadza zopasula oipa;

26 Pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako,Nadzasunga phazi lako lingakodwe.

Malangizo ena osiyana

27 Oyenera kulandira zabwino usawamane;Pokhoza dzanja lako kuwacitira zabwino.

28 Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso,Ndipo mawa ndidzakupatsa;Pokhala uli nako kanthu.

29 Usapangire mnzako ciwembu;Popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.

30 Usakangane ndi munthu cabe,Ngati sanakucitira coipa,

31 Usacitire nsanje munthu waciwawa;Usasankhe njira yace iri yonse.

32 Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova;Koma cinsinsi cace ciri ndi oongoka.

33 Mulungu atemberera za m'nyumba ya woipa;Koma adalitsa mokhalamo olungama.

34 Anyozadi akunyoza,Koma apatsa akufatsa cisomo.

35 Anzeru adzalandira ulemu colowa cao;Koma opusa adzakweza manyazi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31