Miyambi 21 BL92

1 Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi;Aulozetsa komwe afuna.

2 Njira zonse za munthu zilungama pamaso pace;Koma Yehova ayesa mitima.

3 Kucita cilungamo ndi ciweruzoKupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

4 Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza,Ndi nyali ya oipa, ziri cimo.

5 Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu;Koma yense wansontho angopeza umphawi.

6 Kupata cuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.

7 Ciwawa ca amphulupulu cidzawakokolola;Cifukwa akana kucita ciweruzo.

8 Wosenza cimo njira yace ikhotakhota;Koma nchito ya woyera mtima ilungama.

9 Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunikaKuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.

10 Wamphulupulu mtima wace umkhumba zoipa;Sakomera mtima mnzace.

11 Polangidwa wonyoza, wacibwana alandira nzeru,Naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.

12 Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu,Kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa.

13 Wotseka makutu ace polira waumphawi,Nayenso adzalira koma osamvedwa.

14 Mphatso ya m'tseri ipembedza mkwiyo,Ndi mtulo wa pamfunga ukali wolimba.

15 Kucita ciweruzo kukondweretsa wolungama;Koma kuwaononga akucita mphulupulu,

16 Munthu wosocera pa njira ya nzeruAdzakhala m'msonkhano wa akufa.

17 Wokonda zoseketsa adzasauka;Wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

18 Wocimwa ndiye ciombolo ca wolungama;Ndipo waciwembu adzalowa m'malo mwa oongoka mtima.

19 Kukhala m'cipululu kufunikaKuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong'ung'udza.

20 Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta;Koma wopusa angozimeza.

21 Wolondola cilungamo ndi cifundoApeza moyo, ndi cilungamo, ndi ulemu.

22 Wanzeru akwera pa mudzi wa olimba,Nagwetsa mphamvu yace imene anaikhulupirira.

23 Wosunga m'kamwa mwace ndi lilime laceAsunga moyo wace kumabvuto.

24 Wonyada wodzikuza dzina lace ndiye wonyoza;Acita mwaukali modzitama.

25 Cifuniro ca wolesi cimupha;Cifukwa manja ace akana kugwira nchito.

26 Ena asirira modukidwa tsiku lonse;Koma wolungama amapatsa osamana.

27 Nsembe ya oipa inyansa;Makamaka pakudza nayo iwo mwaciwembu.

28 Mboni yonama idzafa;Koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika,

29 Munthu woipa aumitsa nkhope yace;Koma woongoka mtima akonza njira zace.

30 Kulibe nzeru ngakhale lunthaNgakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.

31 Kavalo amakonzedweratu cifukwa ca tsiku la nkhondo;Koma wopulumutsa ndiye Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31