Miyambi 15 BL92

1 Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo;Koma mau owawitsa aputa msunamo.

2 Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa;Koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.

3 Maso a Yehova ali ponseponse,Nayang'anira oipa ndi abwino.

4 Kuciza lilime ndiko mtengo wa moyo;Koma likakhota liswa moyo.

5 Citsiru cipeputsa mwambo wa atate wace;Koma wosamalira cidzudzulo amacenjera.

6 M'nyumba ya wolungama muli katundu wambiri;Koma m'phindu la woipa muli bvuto,

7 Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru,Koma mtima wa opusa suli wolungama.

8 Nsembe ya oipa inyansa Yehova;Koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.

9 Njira ya oipa inyansa Yehova;Koma akonda wolondola cilungamo.

10 Wosiya njira adzalangidwa mowawa;Wakuda cidzudzulo adzafa.

11 Kumanda ndi kucionongeko kuli pamaso pa Yehova;Koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?

12 Wonyoza sakonda kudzudzulidwa,Samapita kwa anzeru.

13 Mtima wokondwa usekeretsa nkhope;Koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima.

14 Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa;Koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru.

15 Masiku onse a wosauka ali oipa;Koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.

16 Zapang'ono, ulikuopa Yehova,Zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso,

17 Kudya masamba, pali cikondano,Kuposa ng'ombe yonenepa pali udani.

18 Munthu wozaza aputa makani;Koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.

19 Mayendedwe a wolesi akunga Hnga laminga,Koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati mseu.

20 Mwana wanzeru akondweretsa atate wace;Koma munthu wopusa apeputsa amace.

21 Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru;Koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ace.

22 Zolingalira zizimidwa popanda upoKoma pocuruka aphungu zikhazikika.

23 Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m'kamwa mwace;Ndi mau a pa nthawi yace kodi sali abwino?

24 Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera,Kuti apambuke kusiya kunsi kwa manda.

25 Yehova adzapasula nyumba ya wonyada;Koma adzalembera mkazi wamasiye malire ace,

26 Ziwembu zoipa zinyansa Yehova;Koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa.

27 Wopindula monyenga abvuta nyumba yace;Koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.

28 Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe;Koma m'kamwa mwa ocimwa mutsanulira zoipa.

29 Yehova atarikira oipa;Koma pemphero la olungama alimvera.

30 Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima;Ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.

31 Khutu lomvera cidzudzulo ca moyoLidzakhalabe mwa anzeru.

32 Wokana mwambo apeputsa moyo wace;Koma wosamalira cidzudzulo amatenga nzeru.

33 Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru;Ndipo cifatso citsogolera ulemu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31