Miyambi 10 BL92

Miyambo yosiyana-siyana; Miyambo ya Sotomo

1 Mwana wanzeru akondweretsa atate;Koma mwana wopusa amvetsa amace cisoni.

2 Cuma ca ucimo sicithangata:Koma cilungamo cipulumutsa kuimfa.

3 Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama;Koma amainga cifuniro ca wocimwa.

4 Wocita ndi dzanja laulesi amasauka;Koma dzanja la akhama lilemeretsa.

5 Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru;Koma wogona pakututa ndi mwana wocititsa manyazi.

6 Madalitso ali pamtu pa wolungamaKoma m'kamwa mwa oipa mubisa ciwawa.

7 Amayesa wolungama wodala pamkumbukira;Koma dzina la oipa lidzabvunda.

8 Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo;Koma citsiru colongolola cidzagwa.

9 Woyenda moongoka amayenda osatekeseka;Koma wokhotetsa njira zace adzadziwika.

10 Wotsinzinira acititsa cisoni;Koma wodzudzula momveka acita mtendere.

11 M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo;Koma m'kamwa mwa oipa mubisa ciwawa.

12 Udani upikisanitsa;Koma cikondi cikwirira zolakwa zonse.

13 Nzeru ipezedwa m'milomo ya wozindikira;Koma wopusa pamsana pace ntyole.

14 Anzeru akundika zomwe adziwaKoma m'kamwa mwa citsiru muononga tsopano lino.

15 Cuma ca wolemera ndi mudzi wace wolimba;Koma umphawi wao uononga osauka.

16 Nchito za wolungama zipatsa moyo;Koma phindu la oipa licimwitsa.

17 Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo;Koma wosiya cidzudzulo asocera.

18 Wobisa udani ali ndi milomo yonama;Wonena ugogodi ndiye citsiru.

19 Pocuruka mau zolakwa sizisoweka;Koma wokhala cete acita mwanzeru.

20 Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika;Koma mtima wa oipa uli wacabe.

21 Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri;Koma zitsiru zimafa posowa nzeru.

22 Madalitso a Yehova alemeretsa,Saonjezerapo cisoni.

23 Masewero a citsiru ndiwo kucita zoipa;Koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.

24 Comwe woipa aciopa cidzamfikira;Koma comwe olungama acifuna cidzapatsidwa.

25 Monga kabvumvulu angopita, momwemo woipa kuti zi;Koma olungama ndiwo maziko osatha.

26 Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso,Momwemo wolesi kwa iwo amene amtuma.

27 Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku;Koma zaka za oipa zidzafinimpha,

28 Ciyembekezo ca olungama ndico cimwemwe;Koma cidikiro ca oipa cidzaonongeka.

29 Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima;Koma akucita zoipa adzaonongeka.

30 Wolungama sadzacotsedwa konse:Koma oipa sadzakhalabe m'dziko.

31 M'kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru;Koma lilime lokhota lidzadulidwa.

32 Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa;Koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota,

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31