Miyambi 19 BL92

1 Wosauka woyenda mwangwiroAposa wokhetsa milomo ndi wopusa.

2 Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino;Ndipo wofulumira ndi mapazi ace amacimwa.

3 Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yace;Mtima wace udandaula pa Yehova.

4 Cuma cionjezetsa mabwenzi ambiri;Koma mnzace wa waumphawi amleka.

5 Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa;Wolankhula mabodza sadzapulumuka.

6 Ambiri adzapembedza waufulu;Ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.

7 Abale onse a wosauka amuda;Nanga mabwenzi ace kodi satanimphirana naye?Awatsata ndi mau, koma kuli zi.

8 Wolandira nzeru akonda moyo wace;Wosunga luntha adzapeza zabwino.

9 Mboni yonama sidzapulumuka cilango;Wolankhula mabodza adzaonongeka.

10 Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;Nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?

11 Kulingalira kwa munthu kucedwetsa mkwiyo;Ulemerero wace uli wakuti akhululukire colakwa.

12 Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango;Koma kukoma mtima kwace kunga mame pamsipu.

13 Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wace;Ndipo makangano a mkazi ndiwo kudontha-donthabe.

14 Nyumba ndi cuma ndizo colowa ca atate;Koma mkazi wanzeru acokera kwa Yehova.

15 Ulesi ugonetsa tulo tofa nato;Ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.

16 Wosunga lamulo asunga moyo wace;Wonyalanyaza mayendedwe ace adzafa.

17 Wocitira waumphawi cifundo abwereka Yehova;Adzambwezera cokoma caceco.

18 Menya mwanako, ciyembekezero ciripo,Osafunitsa kumuononga.

19 Munthu waukali alipire mwini;Pakuti ukampulumutsa udzateronso.

20 Tamvera uphungu, nulandire mwambo,Kuti ukhale wanzeru pa cimariziro cako,

21 Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu;Koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.

22 Cotikondetsa munthu ndico kukoma mtima kwace;Ndipo wosauka apambana munthu wonama.

23 Kuopa Yehova kupatsa moyo;Wokhala nako adzakhala wokhuta;Zoipa sizidzamgwera.

24 Wolesi alonga dzanja lace m'mbale,Osalibwezanso kukamwa kwace.

25 Menya wonyoza, ndipo acibwana adzaceniera;Nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.

26 Wolanda za atate, ndi wopitikitsa amai,Ndiye mwana wocititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.

27 Ukangofuna, mwananga, kusocera kusiya mau akudziwitsa,Leka kumva mwambo.

28 Mboni yopanda pace inyoza ciweruzo;M'kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa,

29 Akonzera onyoza ciweruzo,Ndi mikwingwirima pamsana pa opusa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31