1 Mau a Aguri mwana wa Yake; uthenga. Munthuyo anati, Ndadzitopetsa, Mulungu;Ndadzitopetsa, Mulungu, ndathedwa;
2 Pakuti ndipambana anthu onse kupulukira,Ndiribe luntha la munthu.
3 Sindinaphunzira nzeruNgakhale kudziwa Woyerayo.
4 Ndani anakwera kumwamba natsikanso?Ndani wakundika nafumbata mphepo?Ndani wamanga madzi m'maraya ace?Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko?Dzina lace ndani? dzina la mwanace ndani? kapena udziwa.
5 Mau onse a Mulungu ali oyengeka;Ndiye cikopa ca iwo amene amkhulupirira.
6 Usaoniezere kanthu pa mau ace,Angakudzudzule, nungatsutsidwe kuti ulikunama.
7 Zinthu ziwiri ndakupemphani,Musandimane izo ndisanamwalire:
8 Mundicotsere kutari zacabe ndi mabodza;Musandipatse umphawi, ngakhale cuma,Mundidyetse zakudya zondiyenera;
9 Ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani?Kapena ndingasauke ndi kuba,Ndi kuchula dzina la Mulungu wanga pacabe.
10 Usanamizire kapolo kwa mbuyace,Kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa.
11 Pali mbadwo wotemberera atate ao,Osadalitsa amao.
12 Pali mbadwo wodziyesa oyera,Koma osasamba litsilo lao.
13 Pali mbadwo wokwezatu maso ao,Zikope zao ndi kutukula.
14 Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni;Kuti adye osauka kuwacotsa kudziko, ndi aumphawi kuwacotsa mwa anthu.
15 Msundu uli ndi ana akazi awiri ati, Patsa, patsa,Pali zinthu zitatu sizikhuta konse,Ngakhale zinai sizinena, Kwatha:
16 Manda, ndi cumba,Dziko losakhuta madzi,Ndi moto wosanena, Kwatha.
17 Diso locitira atate wace ciphwete, ndi kunyoza kumvera amace,Makungubwi a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya,
18 Zinthu zitatu zindithetsa nzeru,Ngakhale zinai, sindizidziwa:
19 Njira ya mphungu m'mlengalenga,Njira ya njoka pamwala,Njira ya ngalawa pakati pa nyanja.Njira ya mwamuna ndi namwali.
20 Comweco njira ya mkazi wacigololo;Adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinacita zoipa,
21 Cifukwa ca zinthu zitatu dziko linthunthumira;Ngakhale cifukwa ca zinai silingathe kupirira nazo:
22 Cifukwa ca kapolo pamene ali mfumu;Ndi citsiru citakhuta zakudya;
23 Cifukwa ca mkazi wodedwa wokwatidwa;Ndi mdzakazi amene adzalandira colowa ca mbuyace.
24 Ziripo zinai ziri zazing'ono padziko;Koma zipambana kukhala zanzeru:
25 Nyerere ndi mtundu wosalimba,Koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe.
26 Mbira ndi mtundu wopanda mphamvu,Koma ziika nyumba zao m'matanthwe.
27 Dzombe liribe mfumu,Koma lituruka lonse mabwalo mabwalo.
28 Buluzi ungamgwire m'manja,Koma ali m'nyumba za mafumu.
29 Pali zinthu zitatu ziyenda cinya cinya;Ngakhale zinai ziyenda mwaufulu:
30 Mkango umene uposa zirombo kulimba,Supambukira cinthu ciri conse;
31 Kavalo wolimba m'cuuno, ndi tonde,Ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ace.
32 Ngati wapusa podzikweza,Ngakhale kuganizira zoipa, tagwira pakamwa.
33 Pakuti potakasa mkaka, mafuta ayengekapo;Ndi popsinja mpfuno, mwazi uturukamo;Ndi potimbikira mkwiyo ndeu ionekamo.