Miyambi 1 BL92

Zocitira miyambi

1 MIYAMBI ya Solomo mwana wa Davide, mfumu ya Israyeli.

2 Kudziwa nzeru ndi mwambo;Kuzindikira mau ozindikiritsa;

3 Kulandira mwambo wakusamalira macitidwe,Cilungamo, ciweruzo ndi zolunjika;

4 Kucenjeza acibwana,Kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;

5 Kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira;Ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;

6 Kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lace,Mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.

Munthu asalole oipa amcete

7 Kuopa Yehova ndiko ciyambi ca kudziwa;Opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

8 Mwananga, tamva mwambo wa atate wako,Ndi kusasiya cilangizo ca amako

9 Pakuti izi ndi korona wa cisomo pamtu pako,Ndi mkanda pakhosi pako.

10 Mwananga, akakukopa ocimwa usalole.

11 Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi,Tilalire osacimwa opanda cifukwa;

12 Tiwameze ali ndi moyo ngati manda,Ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;

13 Tidzapeza cuma conse ca mtengo wace,Tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;

14 Udzacita nafe maere,Tonse tidzakhala ndi cibeti cimodzi;

15 Mwananga, usayende nao m'njira;Letsa phazi lako ku mayendedwe ao;

16 Pakuti mapazi ao athamangira zoipa,Afulumira kukhetsa mwazi.

17 Pakuti kuchera msampha pamaso pa mbalame ndi cabe;

18 Ndipo awa abisalira mwazi wao wao, alalira miyoyo yao yao.

19 Mayendedwe a yense wopindula cuma monyenga ngotere;Cilanda moyo wa eni ace,

Ceniezo la Nzeru

20 Nzeru ipfuula panja;Imveketsa mau ace pabwalo;

21 Iitana posonkhana anthu polowera pacipata;M'mudzi inena mau ace;

22 Kodi mudzakonda zacibwana kufikira liti, acibwana inu?Onyoza ndi kukonda kunyoza,Opusa ndi kuda nzeru?

23 Tembenukani pamene ndikudzudzulani;Taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga,Ndikudziwitsani mau anga.

24 Cifukwa ndaitana, ndipo munakana;Ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira;

25 Koma munapeputsa uphungu wangawonse,Ndi kukana kudzudzula kwanga.

26 Inetu ndidzacitiraciphwete tsoka lanu,Ndidzatonyola pakudza mantha anu;

27 Pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula,Ndi pofika tsoka lanu ngati kabvumvulu;Pakudza kwa inu bvuto ndi nsautso.

28 Pamenepo adzandiitana, koma sindidzabvomera;Adzandifunatu, osandipeza ai;

29 Cifukwa anada nzeru,Sanafuna kuopa Yehova;

30 Anakana uphungu wanga,Nanyoza kudzudzula kwanga konse;

31 Momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao,Nadzakhuta zolingalira zao.

32 Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa acibwana kudzawapha;Ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.

33 Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka,Nadzakhala phe osaopa zoipa,

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31