Miyambi 4 BL92

Ceniezo lakuti afune Nzeru nalewe njira za oipa

1 Ananu, mverani mwambo wa atate,Nimuchere makutu mukadziwe luntha;

2 Pakuti ndikuphunzitsani zabwino;Musasiye cilangizo canga.

3 Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga,Wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabala wina.

4 Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine,Mtima wako uumirire mau anga;Sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.

5 Tenga nzeru, tenga luntha;Usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga;

6 Usasiye nzeru, ndipo Idzakusunga;Uikonde, idzakucinjiriza.

7 Nzeru ipambana, tatenga nzeru;M'kutenga kwako konseko utenge luntha.

8 Uilemekeze, ndipo idzakukweza;Idzakutengera ulemu pamene uifungatira.

9 Idzaika cisada ca cisomo pamtu pako;Idzakupatsa korona wokongola.

10 Tamvera mwananga, nulandire mau anga;Ndipo zaka za moyo wako zidzacuruka.

11 Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru,Ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama.

12 Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda;Ukathamanga, sudzapunthwa.

13 Gwira mwambo, osauleka;Uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.

14 Usalowe m'mayendedwe ocimwa,Usayende m'njira ya oipa.

15 Pewapo, osapitamo;Patukapo, nupitirire.

16 Pakuti akapanda kucita zoipa, samagona;Ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwacokera.

17 Pakuti amadya cakudya ca ucimo,Namwa vinyo wa cifwamba.

18 Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kuca,Kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.

19 Njira ya oipa ikunga mdima;Sadziwa cimene ciwapunthwitsa,

20 Mwananga, tamvera mau anga;Cherera makutu ku zonena zanga.

21 Asacoke ku maso ako;Uwasunge m'kati mwa mtima wako.

22 Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza,Nalamitsa thupi lao lonse.

23 Cinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga;Pakuti magwero a moyo aturukamo.

24 Tasiya m'kamwa mokhota,Uike patari milomo yopotoka.

25 Maso ako ayang'ane m'tsogolo,Zikope zako zipenye moongoka,

26 Sinkasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako;Njira zako zonse zikonzeke.

27 Usapatuke ku dzanja lamanja kapena kulamanzere;Suntha phazi lako kusiya zoipa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31