1 Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri,Adzasweka modzidzimuka, palibe comciritsa.
2 Pocuruka olungama anthu akondwa;Koma polamulira woipa anthu ausa moyo.
3 Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wace;Koma wotsagana ndi akazi adama amwaza cuma.
4 Mfumu akhazikitsa dziko ndi ciweruzo;Koma wosonkhetsa anthu mphatso alipululutsa.
5 Wosyasyalika mnzace Acherera mapazi ace ukonde.
6 M'kulakwa kwa woipa muli msampha;Koma wolungama ayimba, nakondwera.
7 Wolungama asamalira mlandu wa osauka;Koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.
8 Anthu onyoza atentha mudzi;Koma anzeru alezetsa mkwiyo.
9 Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa,Ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.
10 Anthu ankhanza ada wangwiro;Koma oongoka mtima asamalira moyowace.
11 Citsiru cibvumbulutsa mkwiyo wace wonse;Koma wanzeru auletsa nautontholetsa.
12 Mkuru akamvera cinyengo,Atumuki ace onse ali oipa,
13 Waumphawi ndi wotsendereza akumana;Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo.
14 Mfumu yolamulira osauka mwantheradi,Mpando wace udzakhazikika kufikira nthawi zonse.
15 Ntyole ndi cidzudzulo zipatsa nzeru;Koma mwana womlekerera acititsa amace manyazi.
16 Pocuruka oipa zolakwa zicuruka;Koma olungama adzaona kugwa kwao.
17 Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa;Nadzasangalatsa moyo wako.
18 Popanda cibvumbulutso anthu amasauka;Koma wosunga cilamulo adalitsika.
19 Kapolo sangalangizidwe ndi mau,Pakuti azindikira koma osabvomera.
20 Kodi uona munthu wansontho m'mau ace?Ngakhale citsiru cidzacenjera, koma ameneyo ai.
21 Yemwe alera kapolo wace mwa ufulu kuyambira ubwana wace,Pambuyo pace adzadziyesa mwana wobala.
22 Mwamuna wamkwiyo aputa makangano;Waukali acuruka zolakwa.
23 Kudzikuza kwa munthu kudzamcepetsa;Koma wokhala ndi mtima wodzicepetsa adzalemekezedwa.
24 Woyenda ndi mbala ada moyo wace wace;Amva kulumbira, koma osaulula kanthu.
25 Kuopa anthu kuchera msampha;Koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka,
26 Ambiri afunafuna ciyanjano ca mkuru;Koma ciweruzo ca munthu cicokera kwa Yehova.
27 Munthu woipa anyansa olungama;Ndipo woongoka m'njira anyansa wocimwa.