Miyambi 13 BL92

1 Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate;Koma wonyoza samvera cidzudzulo.

2 Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwace;Koma moyo wa aciwembu udzadya ciwawa.

3 Wogwira pakamwa pace asunga moyo wace;Koma woyasamula milomo yace adzaonongeka.

4 Moyo wa wolesi ukhumba osalandira kanthu;Koma moyo wa akhama udzalemera.

5 Wolungama ada mau onama;Koma woipa anyansa, nadzicititsa manyazi,

6 Cilungamo cicinjiriza woongoka m'njira;Koma udio ugwetsa wocimwa.

7 Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu;Alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi cuma cambiri.

8 Ciombolo ca moyo wa munthu ndico cuma cace;Koma wosauka samva cidzudzulo.

9 Kuunika kwa olungama kukondwa;Koma nyali ya oipa idzazima.

10 Kudzikuza kupikisanitsa;Koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.

11 Cuma colandiridwa mokangaza cidzacepa;Koma wokundika ndi dzanja adzaona zocuruka.

12 Ciyembekezo cozengereza cidwalitsa mtima;Koma pakufika cifuniroco ndico mtengo wa moyo.

13 Wonyoza mau adziononga yekha;Koma woopa malangizo adzalandira mphotho.

14 Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo,Apatutsa ku misampha ya imfa.

15 Nzeru yabwino ipatsa cisomo;Koma njira ya aciwembu iri makolokoto.

16 Yense wocenjera amacita mwanzeru:Koma wopusa aonetsa utsiru.

17 Mthenga wolakwa umagwa m'zoipa;Koma mtumiki wokhulupirika alamitsa.

18 Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa;Koma wolabadira cidzudzulo adzalemekezedwa.

19 Cifuniro cikondweretsa moyo citacitidwa;Koma kusiya zoipa kunyansa opusa,

20 Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru:Koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.

21 Zoipa zilondola ocimwa;Koma olungama adzalandira mphotho yabwino.

22 Wabwino asiyira zidzukulu zace colowa cabwino;Koma wocimwa angosungira wolungama cuma cace.

23 M'kulima kwa osauka muli zakudya zambiri;Koma zinazo zimaonongeka posowa ciweruzo.

24 Wolekereramwanace osammenya amuda;Koma womkonda amyambize kumlanga.

25 Wolungama adya nakhutitsa moyo wace;Koma mimba ya oipa idzasowa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31