Miyambi 22 BL92

1 Mbiri yabwino ifunika kopambana cuma cambiri;Kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golidi.

2 Wolemera ndi wosauka akumana,Wolenga onsewo ndiye Yehova.

3 Wocenjera aona zoipa, nabisala;Koma acibwana angopitirira, nalipitsidwa.

4 Mphotho ya cifatso ndi kuopa, YehovaNdiye cuma, ndi ulemu, ndi moyo.

5 Minga ndi misampha iri m'njira ya wokhota;Koma wosunga moyo wace adzatarikira imeneyo.

6 Phunzitsa mwana poyamba njira yace;Ndipo angakhale atakalamba sadzacokamo.

7 Wolemera alamulira osauka;Ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.

8 Wofesa zosalungama adzakolola tsoka;Ndipo ntyole ya mkwiyo wace idzalephera.

9 Mwini diso lamataya adzadala;Pakuti apatsa osauka zakudya zace.

10 Ukainga wonyoza, makangano adzaturuka;Makani ndi manyazi adzalekeka.

11 Wokonda kuyera mtima,Mfumu idzakhala bwenzi lace cifukwa ca cisomo ca milomo yace.

12 Maso a Yehova acinjiriza wodziwa;Koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.

13 Waulesi ati, Pali mkango panjapo,Ndidzaphedwa pamakwalalapo.

14 M'kamwa mwa mkazi waciwerewere muli dzenje lakuya;Yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.

15 Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana;Koma ntyole yomlangira idzauingitsira kutari.

16 Wotsendereza waumphawi kuti acurukitse cuma cace,Ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.

Malangizo a pa makhalidwe oyenera munthu

17 Chera makutu ako, numvere mau a anzeru,Nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.

18 Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m'kati mwako,Ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako.

19 Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi,Kuti ukhulupirire Yehova.

20 Kodi sindinakulembera zoposa Za uphungu ndi nzeru;

21 Kuti ukadziwitse ntheradi yace ya mau oona,Nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?

22 Usalande za waumphawi cifukwa ali waumphawi,Ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo.

23 Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao;Omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.

24 Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga;Ngakhale kupita ndi mwamuna waukali;

25 Kuti ungaphunzire mayendedwe ace,Ndi kutengera moyo wako msampha,

26 Usakhale wodulirana mpherere,Ngakhale kumperekera cikole ca ngongole zace.

27 Ngati ulibe cobwezeraKodi acotserenji kama lako pansi pako?

28 Usasunthe cidziwitso cakale ca m'malire,Cimene makolo ako anaciimika.

29 Kodi upenya munthu wofulumiza nchito zace?Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu acabe.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31