Miyambi 8 BL92

Nzeru ipambana m'kucita kwace

1 Kodi nzeru siitana,Luntha ndi kukweza mau ace?

2 Iima pamwamba pa mtunda,Pa mphambano za makwalala;

3 Pambali pa cipata polowera m'mudzi,Polowa anthu pa makomo ipfuula:

4 Ndinu ndikuitanani, amuna,Mau anga ndilankhula kwa ana a anthu.

5 Acibwana inu, cenjerani,Opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira;

6 Imvani, pakuti ndikanena zoposa,Ndi zolungama potsegula pakamwa panga,

7 Pakuti m'kamwa mwanga mudzalankhula ntheradi,Zoipa zinyansa milomo yanga.

8 Mau onse a m'kamwa mwanga alungama;Mwa iwo mulibe zokhota ndi zopotoka.

9 Onsewo amveka ndi iye amene azindikira;Alungama kwa akupeza nzeru.

10 Landirani mwambo wanga, si siliva ai;Ndi nzeru kopambana ndi golidi wosankhika.

11 Pakuti nzeru iposa ngale,Ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo,

12 Ine Nzeru ndikhala m'kucenjera, ngati m'nyumba yanga;Ndimapeza kudziwa ndi zolingalira.

13 Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa;Kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.

14 Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa;Ndine luntha; ndiri ndi mphamvu.

15 Mwa ine mafumu alamulira;Akazembe naweruza molungama.

16 Mwa ine akalonga ayang'anira,Ndi akuru, ngakhale oweruza onse a m'dziko,

17 Akundikonda ndiwakonda;Akundifunafuna adzandipeza.

18 Katundu ndi ulemu ziri ndi ine,Cuma cosatha ndi cilungamo.

19 Cipatso canga ciposa golidi, ngakhale golidi woyengeka;Phindu langa liposa siliva wosankhika.

20 Ndimayenda m'njira ya cilungamo,Pakati pa mayendedwe a ciweruzo,

21 Kuti ndionetse cuma akundikonda, cikhale colowa cao,Ndi kudzaza mosungira mwao.

Nzeru ndiyo ya nthawi yosayamba

22 Mulungu anali nane poyamba njira yace,Asanalenge zace zakale.

23 Anandiimika cikhalire ciyambire,Dziko lisanalengedwe.

24 Pamene panalibe zozama ndinabadwa ine,Pamene panalibe akasupe odzala madzi.

25 Mapiri asanakhazikike,Zitunda zisanapangidwe, ndinabadwa;

26 Asanalenge dziko, ndi thengo,Ngakhale ciyambi ca pfumbi la dziko.

27 Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo;Pamene analemba pazozama kwete kwete;

28 Polimbitsa Iye thambo la kumwamba,Pokula akasupe a zozama.

29 Poikira nyanja malire ace,Kuti madzi asapitirire pa lamulo lace;Polemba maziko a dziko,

30 Ndinali pa mbali pace ngati mmisiri;Ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku,Ndi kukondwera pamaso pace nthawi zonse;

31 Ndi kukondwera ndi dziko lace lokhalamo anthu,Ndi kusekerera ndi ana a anthu.

32 Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,Ngodala akusunga njira zanga.

33 Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.

34 Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku,Ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;

35 Pakuti wondipeza ine apeza moyo;Yehova adzamkomera mnma.

36 Koma wondicimwira apweteka moyo wace;Onse akundida ine akonda imfa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31