Nyimbo 8 BL92

1 Mwenzi utakhala ngati mlongwanga,Woyamwa pa bere la amai!Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona;Osandinyoza munthu.

2 Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai,Kuti andilange mwambo; Ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa,Ndi madzi a makangaza anga.

3 Dzanja lamanzere lace akadanditsamiritsa kumutu,Lamanja lace ndi kundifungatira.

4 Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Muutsiranji, mugalamutsiranji cikondi,Cisanafune mwini.

5 Ndaniyu acokera kucipululu,Alikutsamira bwenzi lace?Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe:Pomwepo amako anali mkusauka nawe,Pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.

6 Undilembe pamtima pako, mokhoma cizindikilo, nundikhomenso cizindikilo pamkono pako;Pakuti cikondi cilimba ngati imfa;Njiru imangouma ngati manda:Kung'anima kwace ndi kung'anima kwa moto,Ngati mphezi ya Yehova,

7 Madzi ambiri sangazimitse cikondi,Ngakhale mitsinje yodzala kucikokolola:Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yace ngati sintho la cikondi,Akanyozedwa ndithu.

8 Tiri ndi mlongwathu wamng'ono,Alibe maere;Ticitirenji mlongwathuTsiku lokhoma unkhoswe wace?

9 Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva:Ngati ndiye citseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.

10 Ndine khoma, maere anga akunga nsanja zace:Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.

11 Solomo anali ndi munda wamipesa ku Baalahamoni;Nabwereka alimi mundawo;Yense ambwezere ndalama cikwi cifukwa ca zipatso zace.

12 Koma munda wanga wamipesa, uli pamaso panga ndiwo wangatu;Naco cikwico, Solomo iwe,Koma olima zipatso zace azilandira mazana awiri.

13 Namwaliwe wokhala m'minda,Anzake amvera mau ako:Nanenso undimvetse.

14 Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga,Dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawalaPa mapiri a mphoka,

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8