1 MASOMPHENYA a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.
2 Imvani, miyamba inu, chera makutu, iwe dziko lapansi, cifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.
3 Ng'ombe idziwa mwini wace, ndi buru adziwa pomtsekereza: koma Israyeli sadziwa, anthu anga sazindikira.
4 Mtundu wocimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakucita zoipa, ana amene acita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israyeli, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.
5 Nanga bwanji mukali cimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.
6 Kucokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe cangwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zironda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.
7 Dziko lanu liri bwinja; midzi yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo liri labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.
8 Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati citando ca m'munda wamphesa, ngati cilindo ca m'munda wamankhaka, ngati mudzi wozingidwa ndi nkhondo.
9 Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.
10 Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, cherani makutu ku cilamulo ca Mulungu wathu, inu anthu a Gomora.
11 Nditani nazo nsembe zanu zocurukazo? ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa ana a nkhosa, ngakhale wa atonde.
12 Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna cimeneci m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga?
13 Musadze nazonso, nsembe zacabecabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano.
14 Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi za mapwando anu mtima wanga uzida; zindibvuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.
15 Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pocurukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.
16 Sambani, dziyeretseni; cotsani macitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kucita zoipa;
17 phunzirani kucita zabwino; funani ciweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.
18 Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.
19 Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,
20 koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; cifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.
21 Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! wodzala ciweruzowo! cilungamo cinakhalamo koma tsopano ambanda.
22 Siliva wako wasanduka mphala, vinyo wako wasanganizidwa ndi madzi.
23 Akuru ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera mirandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.
24 Cifukwa cace Yehova ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israyeli, Ha! ndidzatonthoza mtima wanga pocotsa ondibvuta, ndi kubwezera cilango adani anga;
25 ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzacotsa seta wako wonse:
26 ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga paciyambi; pambuyo pace udzachedwa Mudzi wolungama, mudzi wokhulupirika.
27 Ziyoni adzaomboledwa ndi ciweruzo, ndi otembenuka mtima ace ndi cilungamo.
28 Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ocimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa.
29 Cifukwa adzakhala ndi manyazi, cifukwa ca mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, cifukwa ca minda imene mwaisankha.
30 Cifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lace linyala, ngatinso munda wopanda madzi.
31 Ndimo wamphamvu adzakhala ngati cingwe cabwazi, ndi nchito yace ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.