Yesaya 51 BL92

Israyeli akonzedwanso napulumutsidwa

1 Mverani Ine, inu amene mutsata cilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani ikuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo.

2 Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumcurukitsa.

3 Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ace onse abwinja; ndipo wasandutsa cipululu cace ngati Edene, ndi nkhwangwara yace ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.

4 Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kundicherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzacokera kwa ine, ndipo ndidzakhazikitsa ciweruziro canga cikhale kuunika kwa anthu.

5 Cilungamo canga ciripafupi, cipulumutso canga camuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.

6 Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi pa dziko; pakuti kumwamba kudzacoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati copfunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa cimodzimodzi; koma cipulumutso canga cidzakhala ku nthawi lonse, ndi cilungamo canga sicidzacotsedwa.

7 Mverani Ine, inu amene mudziwa cilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope citonzo ca anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.

8 Pakuti njenjete idzawadya ngati copfunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma cilungamo canga cidzakhala ku nthawi zonse, ndi cipulumutso canga ku mibadwo yonse.

9 Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjiri zipinjiri, amene unapyoza cinjoka cija?

10 Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; amene anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa?

11 Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo cisoni ndi kuusa moyo kudzacoka.

12 Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;

13 waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse cifukwa ca ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? uli kuti ukali wa wotsendereza?

14 Wam'nsinga wowerama adzamasulidwa posacedwa; sadzafa ndi kutsikira kudzenje, cakudya cace sicidzasowa.

15 Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndiutsa nyanja, kuti mafunde ace akokome; Yehova wa makamu ndi dzina lace.

16 Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.

Agalamuke Yerusalemu

17 Galamuka, galamuka, imirira Yerusalemu amene unamwa m'dzanja la Yehova cikho ca ukali wace; iwe wamwa mbale ya cikho conjenjemeretsa ndi kucigugudiza.

18 Palibenso wina wakumtsogolera mwa ana amuna onse, amene iye anawabala; palibe wina amgwira dzanja mwa ana onse anawalera.

19 Izi ziwiri zakugwera; ndani adzakulira iwe? bwinja ndi cipasuko, njala ndi lupanga; ndidzatonthoza mtima wako bwanji?

20 Ana ako amuna akomoka; agona pamtu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako,

21 Cifukwa cace imva ici tsopano, iwe wobvutidwa ndi woledzera koma si ndi vinyo ai;

22 atero Ambuye ako Yehova, ndi Mulungu wako amene anena mlandu wa anthu ace, Taona, ndacotsa m'dzanja mwako cikho conjenjemeretsa, ngakhale mbale ya cikho ca ukali wanga; iwe sudzamwa ico kawirinso.

23 Ndidzaciika m'dzanja la iwo amene abvutitsa iwe; amene anena ku moyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo.