Yesaya 16 BL92

1 Tumizani inu ana a nkhosa kwa wolamulira wa dziko kucokera ku Sela kunka kucipululu, mpaka ku phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.

2 Pakuti ana akazi a Moabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati cisa cofwancuka.

3 Citani uphungu, weruzani ciweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opitikitsidwa, osaulula woyendayenda.

4 Opitikitsidwa a Moabu akhale ndi iwe, khala iwe comphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m'dziko.

5 Ndipo mpando wacifumu udzakhazikika m'cifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m'zoona, m'cihema ca Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa ciweruziro, nadzafulumira kucita cilungamo.

6 Ife tinamva kunyada kwa Moabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwace, ndi kunyada kwace ndi mkwiyo wace; matukutuku ace ali acabe.

7 Cifukwa cace Moabu adzakuwa cifukwa ca Moabu, onse adzakuwa; cifukwa ca maziko a Kirihareseti mudzalira maliro, osautsidwa ndithu.

8 Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibimai; ambuye a mitundu atyolatyola mitengo yosankhika yace; iwo anafikira ngakhale ku Yazeri, nayendayenda m'cipululu; nthambi zace zinatasa, zinapitima panyanja.

9 Cifukwa cace ndidzalira ndi kulira kwa Yazeri, cifukwa ca mpesa wa Sibima, ndidzakukhathamiza ndi misozi yanga, iwe Hesiboni ndi Eleale; cifukwa kuti pa zipatso zako za malimwe, ndi pa masika ako, mpfuu wankhondo wagwera.

10 Ndipo cikondwero ndi msangalalo zacotsedwa m'munda wapatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuyimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mpfuu wa masika amphesa.

11 Cifukwa cace m'mimba mwanga mulirira Moabu, ngati mngoli, ndi za m'mtima mwanga zilirira Kiriheresi.

12 Ndipo padzakhala kuti pamene Moabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika ku malo ace oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.

13 Awa ndi mau amene Yehova adanena za Moabu nthawi zapitazo.

14 Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa nchito, ulemerero wa Moabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikuru lace, ndi otsala adzakhala ang'ongong'ono ndi acabe.