1 Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutari; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anachula dzina langa;
2 nacititsa pakamwa panga ngati lupanga lakuthwa, mu mthunzi wa dzanja lace wandibisa Ine; wandipanga Ine mubvi wotuulidwa; m'phodo mwace Iye wandisungitsa Ine, nati kwa Ine,
3 Iwe ndiwe mtumiki wanga, Israyeli, amene ndidzalemekezedwa nawe.
4 Koma ndinati, Ndagwira nchito mwacabe, ndatha mphamvu zanga pacabe, ndi mopanda pace; koma ndithu ciweruziro canga ciri ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.
5 Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wace, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israyeli asonkhanidwe kwa Iye; cifukwa Ine ndiri wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;
6 inde, ati, Ciri cinthu copepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israyeli; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale cipulumutso canga mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
7 Atero Yehova, Mombolo wa Israyeli, ndi Woyera wace, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyansidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira cifukwa ca Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israyeli, amene anakusankha Iwe.
8 Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la cipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja;
9 ndi kunena kwa iwo amene ali omangidwa, Mukani, kwa iwo amene ali mumdima, Dzionetseni nokha. Iwo adzadya m'njira, ndi m'zitunda zonse zoti se mudzakhala busa lao.
10 Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawacitira cifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.
11 Ndipo ndidzasandutsa mapiri anga onse akhale njira, ndipo makwalala anga adzakwezeka.
12 Taonani, awa adzacokera kutari; ndipo taonani, awa ocokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ocokera ku dziko la Sinimu.
13 Yimbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, yimbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ace, nadzacitira cifundo obvutidwa ace.
14 Koma Ziyoni anati, Yehova wandisiya ine, ndipo Ambuye wandiiwala ine.
15 Kodi mkazi angaiwale mwana wace wa pabere, kuti iye sangacitire cifundo mwana wombala iye? inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.
16 Taona ndakulembera iwe pa zikhato za manja anga; makoma ako alipo masiku onse pamaso panga,
17 Ana ako afulumira; opasula ako ndi iwo amene anakusakaza adzacoka pa iwe.
18 Tukula maso ako kuunguza-unguza, nuone; onsewa asonkhana pamodzi, nadza kwa iwe. Pali Ine, ati Yehova, iwe ndithu udzadzibveka wekha ndi iwo onse, monga ndi cokometsera, ndi kudzimangira nao m'cuuno ngati mkwatibwi.
19 Pakuti, kunena za tnalo ako osiyidwa ndi abwinja ndi dziko lako limene lapasulidwa tsopano, ndithu iwe udzakhala wocepera okhalamo, ndi iwo amene anakumeza iwe adzakhala kutari.
20 Ana ako amasiye adzanena m'makutu ako, Malo andicepera ine, ndipatse malo, kuti ndikhalemo.
21 Pamenepo udzati m'mtima mwako, Ndani wandibalitsa ine amenewa, popeza ana anga anacotsedwa kwa ine, ndipo ndiri wouma, ndi wocotsedwa m'dziko, ndi woyendayenda kwina ndi kwina? ndipo ndani wadza ndi awa? Taona ndinasiyidwa ndekha, amenewa anali kuti?
22 Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakodola anthu a mitundu, ndi kukwezera anthu mbendera yanga; ndipo adzabwera nao ana ako amuna pa cifuwa cao, ndi ana ako akazi adzatengedwa pa mapewa ao.
23 Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao akuru adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka pfumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.
24 Kodi cofunkha cingalandidwe kwa wamphamvu, pena am'nsinga a woopsya angapulumutsidwe?
25 Koma atero Yehova, Ngakhale am'nsinga a wamphamvu adzalandidwa, ndi cofunkha ca woopsya cidzapulumutsidwa; pakuti Ine ndidzakangana naye amene akangana ndi iwe, ndipo ndidzapulumutsa ana ako.
26 Ndipo ndidzadyetsa iwo amene atsendereza iwe ndi nyama yao yao; ndi mwazi wao wao; iwo adzaledzera monga ndi vinyo wotsekemera; anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndiri Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.