Yesaya 26 BL92

Nyimbo yakulemekeza kuciniiriza kwa Yehova

1 Tsiku limenelo adzayimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tiri ndi mudzi wolimba; Iye adzaikacipulumutso cikhale macemba ndi malinga.

2 Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene ucita zoonadi, ulowemo.

3 Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weni weni, cifukwa ukukhulupirirani Inu.

4 Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lacikhalire.

5 Cifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa pfumbi.

6 Phazi lidzaupondereza pansi; ngakhale mapazi a aumphawi, ndi mapondedwe a osowa.

7 Njira ya wolungama iri njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.

8 Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi cikumbukilo canu.

9 Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira cilungamo.

10 Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira cilungamo; m'dziko la macitidwe oongoka, iye adzangocimwa, sadzaona cifumu ca Yehova.

11 Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona cangu canu ca kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamariza adani anu.

12 Yehova, udzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira nchito zathu zonse.

13 Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzachula dzina lanu.

14 Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; cifukwa cace Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa cikumbukiro cao conse.

15 Mwacurukitsa mtundu, Yehova, mwacurukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.

16 Yehova, iwo adza kwa Inu mobvutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.

17 Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yace yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kupfuula m'zowawa zace; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.

18 Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinacite cipulumutso ciri conse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe.

19 Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muyimbe, inu amene mukhala m'pfumbi; cifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzaturutsa mizimu.

20 Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.

21 Pakuti taonani, Yehova adza kucokera ku malo ace kudzazonda okhala pa dziko lapansi, cifukwa ca kuipa kwao; dziko lidzabvumbulutsa mwazi wace, ndipo silidzabvundikiranso ophedwa ace.