1 Katundu wa cigwa ca masomphenya.Mwatani kuti mwakwera nonsenu pamacindwi?
2 Iwe amene wadzala ndi zimpfuu, mudzi waphokoso, mudzi wokondwa; ophedwa ako, sanaphedwa ndi lupanga, sanafe m'nkhondo.
3 Olamulira ako onse athawa pamodzi, anamangidwa ndi amauta; opezedwa ako onse anamangidwa pamodzi, nathawira patari.
4 Comweco ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, cifukwa ca kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,
5 Pakuti ndi tsiku laphokoso, ndi lopondereza pansi, ndi lothetsa nzeru, locokera kwa Ambuye Yehova wa makamu, m'cigwa ca masomphenya, kugumuka kwa malinga, ndi kupfuulira kumapiri.
6 Ndipo Elamu anatenga phodo, ndi magareta a anthu ndi apakavalo; ndipo Kiri anaonetsa zikopa.
7 Ndipo panali kuti zigwa zako zosankhika zinadzala magareta, ndi apakavalo anadzinika okha pacipata.
8 Ndipo Iye anacotsa cophimba ca Yuda; ndipo iwe unayang'ana tsiku limenelo pa zida za m'nyumba ya nkhalango.
9 Ndipo inu munaona kuti pa mudzi wa Davide panagumuka mipata yambiri; ndipo munasonkhanitsa pamodzi madzi a m'thamanda lakunsi.
10 Ndipo inu munawerenga nyumba za Yerusalemu, ndipo munagwetsa nyumba, kuti mumangire linga.
11 Inu munapanganso cosungamo madzi a thamanda lakale, pakati pa malinga awiri; koma inu simunamuyang'ane iye amene anacicita ico, ngakhale kusamalira iye amene analipanga kale.
12 Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kubvala ciguduli m'cuuno;
13 koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, cifukwa mawa tidzafa.
14 Ndipo Yehova wa makamu wadzibvumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu coipa cimeneci sicidzacotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu.
15 Atero Ambuye Yehova wa makamu, Muka, pita iwe kwa kapitao uyu, kwa Sebina woyang'anira nyumba, ndi kuti,
16 Ucitanji iwe kuno, ndimo ndani ali nawe kuno, kuti iwe wagoba manda kuno, ndi kudzigobera manda pamwamba, ndi kudzisemera mogonamo m'thanthwe.
17 Taona Yehova adzakuponya iwe zolimba, monga mwamuna wamphamvu, inde adzakufumbata zolimba.
18 Iye ndithu adzakuzunguza, ndi kukuponyaponya ngati mpira m'dzido lalikuru; kumeneko iwe udzafa, ndipo kumeneko kudzakhala magareta a ulemerero wako, iwe wocititsa manyazi banja la mbuye wako.
19 Ndipo Ine ndidzakuturutsa iwe mu nchito yako, ndi kukutsitsa iwe pokhala pako.
20 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ine ndidzaitana mtumiki wanga, Eliakimu mwana wa Hilikiya:
21 ndipo ndidzambveka iye cobvala cako, ndi kumlimbikitsa ndi lamba lako, ndipo ndidzapereka ulamuliro wako m'dzanja lace; ndipo iye adzakhala atate wa okhala m'Yerusalemu ndi a nyumba ya Yuda.
22 Ndipo ndidzaika mfungulo wa nyumba ya Davide paphewa pace, ndipo iye adzatsegula, ndipo palibe wina adzatseka, iye adzatseka ndipo palibe wina adzatsegula.
23 Ndipo ndidzamkhomera iye ngati msomali polimba; ndipo iye adzakhala mpando wa ulemerero wa banja la atate wace.
24 Ndipo iwo adzapacika pa iye ulemerero wonse wa banja la atate wace, obadwa ndi ana, mbiya zonse zazing'ono, ngakhale zikho ndi aguda omwe.
25 Tsiku limenelo, ati Yehova wa makamu, msomali wokhomeredwa polimba udzasukusika; nudzaguluka, ndi kugwa, ndi katundu wopacikidwapo adzadulidwa; pakuti Yehova wanena.