Yesaya 42 BL92

Mtumiki wa Yehova

1 Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzaturutsira amitundu ciweruziro.

2 Iye sadzapfuula, ngakhale kukuwa, pena kumvetsa mau ace m'khwalala.

3 Bango lophwanyika sadzalityola, ndi lawi lozirala sadzalizima; adzaturutsa ciweruzo m'zoona.

4 Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa ciweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira cilamulo cace.

5 Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi cimene cituruka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;

6 Ine Yehova ndakuitana Iwe m'cilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;

7 kuti utsegule maso akhungu, uturutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, aturuke m'nyumba ya kaidi.

8 Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.

9 Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizichula; zisanabuke ndidzakumvetsani.

10 Yimbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ace kucokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse ziri m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.

11 Cipululu ndi midzi yace ikweze mau ao, midzi imene Kedara akhalamo; okhala m'Sela ayimbe, akuwe kucokera pamwamba pa mapiri.

12 Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ace m'zisumbu.

13 Yehova adzaturuka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzapfuula, inde adzakuwa zolimba; adzacita zamphamvu pa adani ace.

14 Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula; ndakhala cete ndi kudzithungata ndekha; tsopano ndidzapfuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.

15 Ndidzapasula mapiri ndi zitunda, ndi kuumitsa zitsamba zao zonse; ndi kusandutsa nyanja zisumbu, ndi kuumitsa matamanda.

16 Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa; m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu Izi ine ndidzacita, ndipo sindidzawasiya.

17 Iwo adzabwezedwa m'mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu.

18 Imvani, agonthi inu; yang'anani, akhungu inu, kuti muone.

19 Ndani ali wakhungu, koma mtumiki wanga? pena wagonthi, monga mthenga wanga, amene ndimtumiza? ndani ali wakhungu monga bwenzi langa, ndi wakhungu monga mtumiki wa Yehova?

20 Iwe waona zinthu zambiri, koma susamalira konse; makutu ako ali otseguka, koma sumva konse.

21 Cinakondweretsa Yehova cifukwa ca cilungamo cace kukuza cilamulo, ndi kucilemekeza.

22 Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m'mauna, nabisidwa m'nyumba zakaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani.

23 Ndani mwa inu adzachera khutu lace pamenepo? amene adzamvera ndi kumva nthawi yakudza?

24 Ndani anapereka Yakobo, kuti afunkhidwe, ndi Israyeli, kuti awawanyidwe? kodi si Yehova? Iye amene tamcimwira, ndi amene iwo anakonda kuyenda m'njira zace, ngakhale kumvera ciphunzitso cace.

25 Cifukwa cace anatsanulira pa iye mkwiyo wace waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwace, koma iye sanadziwa; ndipo unamtentha, koma iye sanacisunga m'mtima.