1 Caka cimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wacifumu wautari, ndi wotukulidwa, ndi zobvala zace zinadzala m'Kacisi.
2 Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yace, awiri naphimba nao mapazi ace, awiri nauluka nao.
3 Ndipo wina anapfuula kwa mnzace, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wace.
4 Ndipo maziko a ziundo anasunthika ndi mau amene anapfuula, ndipo nyumba inadzazidwa ndi utsi.
5 Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! cifukwa ndathedwa; cifukwa ndiri munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; cifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.
6 Pompo anaulukira kwa ine mmodzi wa aserafi, ali nalo khala lamoto m'dzanja mwace, limene analicotsa ndi mbaniro pa guwa la nsembe;
7 nakhudza nalo kukamwa kwanga nati, Taona ici cakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zacotsedwa, zocimwa zako zaomboledwa.
8 Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.
9 Ndipo Iye anati, Kauze anthu awa, Imvani inu ndithu, koma osazindikira; yang'anani inu ndithu, koma osadziwitsa.
10 Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, naciritsidwe.
11 Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka midzi ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu,
12 ndipo Yehova wasunthira anthu kutari, ndi mabwinja adzacuruka pakati pa dziko.
13 Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kacere, ndi monganso thundu, imene tsinde lace likhalabe ataigwetsa; cotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lace.