1 Koma kumene kunali nsautso sikudzakhala kuziya. Poyamba paja Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni, ndi dziko la Naftali, koma potsiriza pace Iye analicitira ulemu, pa khwalala la kunyanja, patsidya pa Yordano, Galileya wa amitundu.
2 Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukuru; iwo amene anakhala m'dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwaturukira kwa iwo.
3 Inu mwacurukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.
4 Pakuti gori la katundu wace, ndi mkunkhu wa paphewa pace, ndodo ya womsautsa, inu mwazityola monga tsiku la Midyani.
5 Pakuti zida zonse za mwamuna wobvala zida za nkhondo m'phokosomo, ndi zobvala zobvimvinika m'mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni.
6 Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
7 Za kuenjezera ulamuliro wace, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wacifumu wa Davide, ndi pa ufumu wace, kuukhazikirsa, ndi kuucirikiza ndi ciweruziro ndi cilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Cangu ca Yehova wa makamu cidzacita zimenezi.
8 Ambuye anatumiza mau kwa Yakobo, ndipo anatsikira pa Israyeli.
9 Ndipo anthu onse adzadziwa, ngakhale Efraimu ndi okhala m'Samariya, amene anena m'kunyada ndi m'kukula kwa mtima,
10 Njerwa zagwa, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema; mikuyu yagwetsedwa, koma tidzaisinthanitsa ndi mikungudza.
11 Cifukwa cace Yehova adzamkwezera Rezini olimbana naye, nautsa adani ace;
12 Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israyeli ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.
13 Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu.
14 Cifukwa cace Yehova adzadula mutu wa Israyeli ndi mcira wace; nthambi ya kanjedza ndi mlulu, tsiku limodzi.
15 Nkhalamba ndi wolemekezeka ndiye mutu, ndi mneneri wophunzitsa zonama ndiye mcira.
16 Pakuti iwo amene atsogolera anthuwa, ndiwo awasokeretsa; ndipo iwo amene atsogoleredwa nao aonongeka.
17 Cifukwa cace Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwacitira cifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wocimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.
18 Pakuti kucimwa kwayaka ngati moto kumariza lunguzi ndi minga, inde kuyaka m'nkhalango ya m'thengo, ndipo zifuka capamwamba, m'mitambo yautsi yocindikira.
19 M'kukwiya kwa Yehova wa makamu, dziko latenthedwa ndithu, anthunso ali ngati nkhuni; palibe munthu wocitira mbale wace cisoni.
20 Ndipo wina adzakwatula ndi dzanja lamanja, nakhala ndi njala; ndipo adzadya ndi dzanja lamanzere, osakhutai; iwo adzadya munthu yense nyama ya mkono wace wa iye mwini.
21 Manase adzadya Efraimu ndi Efraimu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.