Yesaya 37 BL92

Mwa mantha Hezekiya aitana mnenert Yesaya

1 Ndipo panali pamene mfumu Hezekiya anamva, anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli, nalowa m'nyumba ya Yehova.

2 Ndipo anatumiza Eliakimu, wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi akuru a nsembe, atapfunda ciguduli, kwa Yesaya, mneneri, mwana wa Amozi.

3 Ndipo iwo anati kwa iye, Hezekiya atere, Tsiku lalero ndilo tsiku la bvuto, ndi lakudzudzula, ndi citonzo; pakuti nthawi yace yakubala ana yafika, ndipo palibe mphamvu yobalira.

4 Kapena Yehova Mulungu wako adzamva mau a kazembeyo, amene mfumu ya Asuri mbuyace inamtuma kukatonza Mulungu wamoyo, nadzadzudzula mau amene Yehova Mulungu wako adawamva; cifukwa cace, kweza pemphero lako cifukwa ca otsala osiyidwa.

5 Ndipo atumiki a mfumu Hezekiya anadza kwa Yesaya.

6 Ndipo Yesaya anati kwa iwo, Mukati kwa mbuyanu, Atero Yehova, musaope mau amene wawamva iwe, amene atumiki a mfumu ya Asuri andilalatira Ine.

7 Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko la kwao.

Uthenga wa Sanakeribu wa kwa Hezekiya

8 Ndipo kazembeyo anabwerera, napeza mfumu ya Asuri irikuponyana nkhondo ndi Libina; pakuti anamva kuti inacoka ku Lakisi.

9 Ndipo anamva anthu alinkunena za Tiraka, mfumu ya Kusi, Iye waturuka kudzamenyana ndi iwe. Ndipo pamene anamva, iye anatumiza mithenga kwa Hezekiya ndi kuti,

10 Mukati kwa Hezekiya, mfumu ya Yuda, Asakunyenge Mulungu wako, amene iwe umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sadzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asuri.

11 Taona, iwe wamva cimene mafumu a Asuri anacitira maiko onse, ndi kuwapasula konse; ndipo kodi iwe udzapulumutsidwa?

12 Kodi milungu ya amitundu yaipulumutsa iyo, imene atate anga anaipasula? Gozani ndi Harani ndi Rezefi ndi ana a Edeni amene anali m'Telasara.

13 Iri kuti mfumu ya ku Hamati, ndi mfumu ya ku Aripadi, ndi mfumu yamudzi wa ku Sefaravaimu, ya ku Hena, ndi Iveva?

Pemphero la Hezekiya

14 Ndipo Hezekiya analandira kalatayo m'manja mwa mithengayo, namuwerenga; ndipo Hezekiya anakwera kunka ku nyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.

15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova, nati,

16 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

17 Cherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Sanakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.

18 Zoonadi, Yehova, mafumu a Asuri anaononga maiko onse, ndi pokhala pao.

19 Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma nchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; cifukwa cace iwo anaiononga,

20 Cifukwa cace, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwace, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.

Kuyankha kwa Yehova mwa Yesaya

21 Ndipo Yesaya, mwana wa Amozi, anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Popeza wandipemphera za Sanakeribu mfumu ya Asuri,

22 awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi ciphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wace pambuyo pako.

23 Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? ndiye Woyera wa Israyeli.

24 Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magareta anga ine ndafika ku nsonga za mapiri, ku mbali za Lebano; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pace penipeni, ku nkhalango ya munda wace wobalitsa.

25 Ine ndakumba ndi kumwa madzi, ndidzaumitsa nyanja zonse za Aigupto ndi kuphazi kwanga.

26 Kodi iwe sunamve, kuti ndinacita ici kale, ndi kucikonza nthawi zakale? tsopano Ine ndacikwaniritsa, kuti iwe ukapasule midzi yamalinga, isanduke miunda.

27 Cifukwa cace okhalamo analefuka, naopsedwa, nathedwa nzeru; ananga udzu wa in'munda, ndi masamba awisi, ndi udzu wa pamacindwi, ndi munda wa tirigu asanakule.

28 Koma ndidziwa pokhala pansi pako, ndi kuturuka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundikwiyira kwako.

29 Cifukwa ca kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m'makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m'mphuno mwako, ndi capakamwa canga m'milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m'njira yomwe unadzerayo.

30 Ndipo ici cidzakhala cizindikilo kwa iwe: caka cino mudzadya zimene ziri zomera zokha, ndipo caka caciwiri mankhokwe ace; ndipo caka cacitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yamphesa ndi kudya cipatso cace.

31 Ndipo otsala amene opulumuka a nyumba ya Yuda adzaphukanso mizu pansi, nadzabala cipatso pamwamba.

32 Pakuti mudzaoneka m'Yerusalemu, otsala ndi opulumuka m'Yerusalemu, otsala ndi opulumuka m'phiri la Ziyoni; cangu ca Yehova wa makamu cidzacita ici.

33 Cifukwa cace atero Yehova za mfumu ya Asuri, Iye sadzafika pa mudzi uno, ngakhale kuponyapo mubvi, ngakhale kufika patsogolo pace ndi cikopa, ngakhale kuunjikirapo mulu.

34 Pa njira yomwe anadzerayo, abwerera yomweyo, ndipo sadzafika pa mudzi uno, ati Yehova.

35 Pakuti ndidzacinjiriza mudzi uno, kuupulumutsa, cifukwa ca Ine mwini, ndi mtumiki wanga Davide.

36 Ndipo mthenga wa Yehova anaturuka, naphaipha m'zitando za Asuri, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.

37 Ndipo Sanakeribu, mfumu ya Asuri, anacoka, namuka, nabwerera, nakhala pa Nineve,

38 Ndipo panali, pamene iye analikupembedzera m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wace, Adrameleki ndi Sarezeri, ana ace anampha iye ndi lupanga; ndipo iwo anapulumuka, nathawira ku dziko la ku Ararati. Ndipo Esaradoni, mwana wace, analamulira m'malo mwace.