1 Iwo amene sanafunsa za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaira andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunachula dzina langa.
2 Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m'njira mosati mwabwino, kutsata maganizo ao ao;
3 anthu amene andiputa Ine kumaso kwanga nthawi zonse, apereka nsembe m'minda, nafukizira zonunkhira panjerwa;
4 amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;
5 amene ati, Ima pa wekha, usadze cifupi ndi ine, pakuti ine ndiri woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.
6 Taonani, calembedwa pamaso panga; sindidzakhala cete, koma ndidzabwezera, inde ndidzabwezera pa cifuwa cao,
7 zoipa zanu zanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandicitira mwano pazitunda; cifukwa cace Ine ndidzayesa nchito yao yakale ilowe pa cifuwa cao.
8 Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, momwemo ndidzacita cifukwa ca atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.
9 Ndipo ndidzaturutsa mbeu mwa Yakobo, ndi mwa Yuda wolowa nyumba wa mapiri anga; ndipo osankhidwa anga adzalandira colowa cao, ndi atumiki anga adzakhala kumeneko.
10 Ndipo Saroni adzakhala podyetsera nkhosa, ndi cigwa ca Akori cidzakhala pogona zoweta kwa anthu anga amene andifuna Ine.
11 Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mlungu wamwai gome, ndi kudzazira mlungu waimfa zikho za vinyo wosanganiza;
12 ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munacita coipa m'maso mwanga, ndi kusankha cimene Ine sindinakondwera naco.
13 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi;
14 taonani, atumiki anga adzayimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wacisoni; ndipo mudzapfuula cifukwa ca kusweka mzimu.
15 Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale citemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzacha atumiki ace dzina lina;
16 comweco iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zobvuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.
17 Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwa tsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.
18 Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ici ndicilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ace okondwa.
19 Ndipo ndidzasangalala m'Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akupfuula.
20 Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ace; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wocimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatembereredwa.
21 Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzanka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zace.
22 Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzanka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhalamasiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi nchito za manja ao.
23 Iwo sadzagwira nchito mwacabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbeu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa ao adzakhala pamodzi ndi iwo.
24 Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali cilankhulire, Ine ndidzamva.
25 Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi pfumbi lidzakhala cakudya ca njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.