Yesaya 47 BL92

Babulo adzaonongeka konse

1 Tsika, ukhale m'pfumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babulo; khala pansi popanda mpando wacifumu, mwana wamkazi wa Akasidi, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.

2 Tenga mipero, nupere ufa; cotsa cophimba cako, bvula copfunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje.

3 Marisece ako adzakhala osapfundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzacita kubwezera, osasamalira munthu.

4 Mombolo wathu, Yehova wa makamu ndi dzina lace, Woyera wa Israyeli.

5 Khala iwe cete, lowa mumdima, mwana wamkazi wa Akasidi; pakuti sudzachedwanso mkazi wa maufumu.

6 Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa colowa canga, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsera cifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.

7 Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalira izi mumtima mwako, kapena kukumbukira comarizira cace.

8 Cifukwa cace tsono, imva ici, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana;

9 koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa unyinji wa matsenga ako, ndi pakati pa maphenda ako ambirimbiri.

10 Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi cidziwitso cako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina.

11 Cifukwa cace coipa cidzafika pa iwe; sudzadziwa kuca kwace, ndipo cionongeko cidzakugwera; sudzatha kucikankhira kumbali; ndipo cipasuko cosacidziwa iwe cidzakugwera mwadzidzidzi.

12 Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira nchito ciyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.

13 Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam'mwamba, oyang'ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera.

14 Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha ku mphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako.

15 Zinthu zomwe unagwira nchito yace, zidzatero nawe; iwo amene anacita malonda ndi iwe ciyambire pa ubwana wako, adzayenda yense kunka kumalo kwace; sipadzakhala wopulumutsa iwe.